Mutu 2

1 Ine ndine duwa ya ku Sharoni, kakombo wa muzigwa. 2 Ngati kakombo pakati pa minga, chamene icho chikondi changa pakati pa asikana. 3 Monga mutengo wa apulikoti pakati pa mitengo ya munkalango, chimozimozi okondewa wanga pakati pali bamuna. Nimankala pansi pachifile chake mosangalala kwambili, ndipo zipaso zake ni zozuna pakumvala kwanga. 4 Ananibwelesa kunyumba ya vinyu, ndipo chikwangwani chake pali ine chinali chikondi. 5 Nsisimuseni ine makeke a mphesa ndipo munisisimuse na ma apulikoti, chifukwa nalema na chikondi. 6 Kwanja kwake kwamanzele kuli pansi kwa mutu wanga, ndipo kwanja kwake kwamanja kwanikumbatila ine. 7 Nifuna niku lumbile, mwana mukazi iwe waku Yelusalemu, na mphoyo na nswala zamusanga , kuti simuzausha kapena kuusha chikondi kufikila akakondwela. 8 Pali phokoso pali okondewa wanga! Mvelani, apa abwela, akudumpha pamapili, nakujumpha pamapili. 9 Okondewa wanga ali kwati mbawala kapena mwana wa mphoyo; onani, wayimilila kuseli kwa khoma yathu, akuyang'anisisa pazenela, asuzumila pazenela. 10 Okondewa wanga anani kambisa kuti, uka, okodewa wanga; okongola wanga, tiye, 11 Ona, mpepo yapita; mvula yapita, yayenda. 12 Maluwa yaonekela paziko ya pansi; ntawi yodulia na kuimba kwa nyoni yafika, ndipo phokoso ya nkunda ya mveka mu ziko yatu. 13 Mutengo wa mukuyu yapya nkuyu wake yobiliwila, ndipo mipesa yachita maluba; zipeleka fungo yake. Nyamuka, okodewa wanga, okongola wanga, tiye tiziyenda. 14 Nkunda yanga, muma tantwe ya thanthwe, muchisinsi ca mumatanthwe chamuma pili yobisamilako, chifukwa mawu yako ni ya niyozuna, ndipo pa menso pako ni pokongola. " 15 Gwila ka nkandwe, ka nkandwe ka ngono kamene kaononga minda ya mphesa, chifukwa munda watu wamphesa uli na maluba. 16 Okondewa wanga ni wanga, ndipo ine ndine wake; adyela pakati pa maluba mwachisangalalo 17 Yenda, okondewa wanga, mphepo yamutandakucha isanabwele na chiuviliuvili chisana yende . Chokani; nkala kwati mphoyo, kapena nswala pa mapili yolimba.