1 Nyimbo yokwezeka. nizakweza menso yanga kumapili; Tandizo yanga izachokela kuti? 2 Tandizo yanga ichokela kuli Yehova, wamene anapanga kumwamba na ziko lapansi. 3 Sazavomeleza kwendo yako kushelemuka; iye wamene amakuchingiliza sazakusila. 4 Ona, woyanganila Israeli sakusila kapena kugona. 5 Yehova ndiye okuyanganilani; Yehova ndiye mutunzi ku kwanja yako yamanja. 6 zuba sizaku ocha muzuba, ngankale mwezi usiku. 7 Yehova azakuchingiliza kuchokela ku zoipa zonse, ndipo azachingiliza umoyo wako. 8 Yehova azakuchingiliza muli vonse vamene uchita manje namuyayaya.