Mutu 114

1 Pamene Israyeli anachoka mu Igupto, nyumba ya Yakobo kuchokela kuli bantu okamba chinenelo chacilendo, 2 Yuda ana nkala malo yake yoyela, Israyeli ufumu wake. 3 Nyanja inayangana naku taba; Yordano ina tembenuka. 4 Mapili yana jumpa kwati nkosa za mpongo, vitunda vina jumpa kwati bana ba nkosa. 5 Watabila chani nyanja iwe? Yordani, yabwelela chifukwa chani? 6 Mapili, wa jumpa bwanji kwati nkosa zampongo? Imwe mapili, mujumpa bwanji kwati bana ba nkosa? 7 njenjeme, ziko yapansi, pa menso pa Yehova, pa menso pa Mulungu wa Yakobo. 8 Bana sandusa mwala ku nkala tamanda ya manzi, mwala yolimba ku nkala kasupe wa manzi.