1
paulo, kaidi wa yesu khristu, ni m'bale timoteyo kwa filimoni, mnzathu ogwira naye nchito,
2
ni apphia mulongo, ni kwa archippus msilikali mnzathu, na kwa mpingo wamene ukumana mu nyumba mwako.
3
Chisomo chinkhale na inu ni mtendere wa kwa mulungu atate wathu na ambuye yesu khristu.
4
nimamuyamika mulungu wanga nthawi zonse. nimakukumbukani mu mapempero yanga.
5
namvera za chikondi chamene muli nacho pali ambuye yesu na bonse bokulupilika.
6
nipempera kuti kunkhala kwanu pamozi kwa chikulupiliro kunkhale kolimba pa kuziwa zonse zabwino zamene zili pakati kathu mwa khristu.
7
chifukwa ninali na chimwemwe chachikulu chifukwa cha chikondi chanu, chifukwa mitima za okulupilira yalandira zabwino kuchokera kwa iwe, m'bale.
8
kotero, ngankhale nili na chilimbiso chonse mwa yesu khristu yokuwuzani zamene muyenera kuchita,
9
koma kamba ka chikondi, nikupemphani mumalo mwake- ine, paulo, munthu okalamba, tsopano kaidi wa yesu khristu.
10
nikufunsani za mwana wanga onesimus, wamene ninabala mu zingwe.
11
chifukwa poyamba anali opanda nchito kwa inu, koma sopano ali na nchito kwa inu na ine.
12
namutuma kwa inu, wamene ni mutima wanga.
13
ninakakonda kumusunga pamozi na ine kuti anigwirire nchito m'malo mwa inu, pamene nili mu zingwe kamba ka uthenga wabwino.
14
koma sininafune kuchita chilichonse popanda maganizo yanu. sininafune nchito zanu za bwino kuti zinkhale kamba ka zichitidwe koma kuchoka pa kufuna kwa bwino.
15
mwina mwa ichi anatengewa kuchoka kuli inu kwa ka nthawi kuti munkhale naye muyayaya.
16
sazankhalaso kapolo, koma opambana kapolo, m'bale okondedwa. ni okondedwa maka-maka kwa ine, komanso kwa inu, mu thupi komanso mwa ambuye.
17
kotero ngati muli na ine monga bwenzi, mulandileni monga ine.
18
ngati wina wakulakwisani kapena ali nanu ngongole iliyonse, munipase ine mulandu.
19
ine, paulo, nilemba izi na kwanja yanga: nizakulipilani. osakuuzani kuti muli na ngongole kwa inu nokha.
20
inde, m'bale, nikomeleni mtima mwa ambuye; lekani mtima wanga upumule mwa khristu.
21
nikulupilira kugonjera kwanu, nikulemberani. niziba muzachita kuchila vamene nakupemphani.
22
pa nthawi imozi, konzani chipinda cha ine, chifukwa nili na chikulupiliro kuti kupyolera mu mapemphero yanu nizabwerera kwa inu.
23
epaphras, kaidi munzanga mwa yesu khristu yesu, akupasani moni.
24
nayeve marko, aristarchus, demas na luka, banchito banzanga.
25
chisomo cha ambuye yesu khristu chinkhale ni mizimu yanu. amen.