Mutu 9

1 Ndipo anati kwa iwo, "Zoonadi ndinena kwa inu, alipo pano mwainu wamene sazalawapo ifa akalibe kuonapo ufumu wa Mulungu ulikusika mwa mpamvu." 2 Patapita cabe masiku sikisi, Yesu anathenga Petulo ndi Yakobo ndi Yohana, kuluphiri, yeka ndi iwo cabe. Ndipo anayaluka pali iwo. 3 Covala cake cinayela ndi kung'anima, kwambiri, cinayela kupambana ciliconse pano pa ziko lapansi. 4 Naye Eliya ndi Mose anaonekela kwa iwo, ndipo anali kulankhula ndi Yesu. 5 Petulo anayankha ndikunena kwa Yesu, " Rabbi, cili bwino cabe kuli ife kuti tinkhalilile kuno, telo tiyeni timange misasa itatu, imozi ya Mose, ndi imozi ya Eliya." 6 (Koma sanaziwe conena cifukwa anali ndi mantha,) 7 Makumbi anabwela ndi kuwavinikila iwo. Ndipo mau anacokela mumakumbi, "Uyu ndimwana wanga wokondedwa. Mveleni iye." 8 Mozizimuka, pamene anaona- ona, sanaone munthu wina aliyense pafupi ndi iwo, koma Yesu cabe. 9 Pamene analikuseluka luphiri, anawalamulila kuti asauze munthu aliyense camene anaona, kufikira pameneMwana wa Munthu atauka kwa kufwa. 10 Ndipo anasunga ici cinthu kwa iwo cabe, koma analankhulapo pakati pawo cabe, " kuuka kwa kufa" Kutanthauza cani 11 Anamfunsa iye nati, "Cifukwa cani alembi akunena kuti Eliya afunika kubwela coyamba?" 12 Anati kwa iwo, "Eliya afunika kubwela coyamba kuti aze aze aike m'malo mwake zinthu zonse. Nanga, cifukwa cani kunalembewa kuti Mwana wa Munthu afunika kusausidwa kuzinthu zambiri ndi kumuyesa ngati alibe nchito kawaya-waya? 13 Koma ndikuuzani kuti Eliya anabwela, ndipo anamcitila ciliconse camene anafuna, ngani mwamalembo mwamene anenela za iye." 14 Pamene anabwela kwa wophunzira ake, anaona anthu ambiri alipafupi ndi alembi alikususana nawo. 15 Koma pamene anamuona iye, anthu wonse anadabwa ndipo anamutamangila iye ndikukampasa moni iye. 16 Anawafunsa wophunzila ake, "kodi mulikususana ciyani?" 17 Munthu wina mucigulu ca anthu anayankha nati, " Mphunzisi, ndinabwela naye mwana wanga kwa inu. Ali na cimzimu camene cimamulesa kukamba. 18 Nthawi zina cimamupaya ndikumugwesa pansi ndi povu kukamwa, ndikusheta menu, ndipo amauma. Ndinapempha wophunzira anu kuti acicose, koma alephela." 19 Anayankha iwo nati, " Mutundu wosakhulupirila, kodi ndizakhala nau kufikira liti? Kodi ndizakulolani kufikira liti? Muleteni kwa ine." 20 Anamubwelesa munyamata kwa iye. Pamene mzimu unaona Yesu, Panthawi yamene ija unamugwesa pansi ndikumba kukunyuka. M'nyamata anagwa pansi ndi povu kukamwa. 21 Yesu anafunsa atate ake, "Kodi ankhala so kwa zaka zinganti?" Atate ake anayankha, " Kucokela ku umwana wake. 22 Cankhala nthawi zina kumuponyela ku moto kapena ku manzi kufunisisa kuti cimuononge iye. ngati mungakwanishe kumtandiza napapata mucitileni cifundo, mutandizeni." 23 Yesu anati kwa iye, "Ngati mukwanisha?' Zinthu zonse zitheka kuli wonse amene akhulupirira." 24 Panthawi yamene iyo atate a mwana analira ndi kunena, " Ndikulupirira! Ndithandizeni kusakhulupirira kwanga!" 25 Pamene Yesu anaona anthu ambiri alikuthamangira kwa iwo, anazuzula mizimu yonyansa ndi kuti, "Iwe cimuzimu cosalankhula ndi cosamvela, ndikulamulira, coka muli uyu, ndipo usakabwelenso muli uyu munthu." 26 Cinalira kwambiri ndikumukunyula mnyamata. Mnyamata anaoneka kwati wakomoka, ndipo ambiri anati, "wafa" 27 Koma Yesu anamnyamula pa kwanja ndikumuimiririka, ndipo mnyamata anaimirira. 28 Pamene Yesu anangena munyumba, wophunzila ake anamfunsa kumbali nati, "Cifukwa nicani ife sitinakwanishe kucicosa ?" 29 Iye anati kwa iwo, "Ici camutundu wa so sicingacoke cabe koma na Pemphelo." 30 Anacoka malo aja ndi kupitirira Galileya. Sanafune kuti wonse aziwe kwamene analili, 31 cifukwa analikuphunzisa wophunzila ake. Anati kwa iwo, "Mwana wa Munthu azapelekedwa mumanja ya anthu, ndipo azamupaya. Akazamupaya, pazapita cabe masiku atatu azaukanso." 32 Koma sanamvesese mau aya, ndipo anali ndi manta kumfunsa iye. 33 anaza kukapenauni. ndipo paemene anali m'nyumba anawafunsa iwo, "Kodi munali kulankhula cani mnjira?" 34 koma anali cete. Cifukwa anali kususana pakati kawo m'njira kuti wamkulu ni ndani? 35 Anankhala pansi ndikuitana aja twelufu pamozi, ndi kuwauza aja, " Ngati pali wina amene afuna kukhala woyamba, afunika kunkhala wotela pa wonse ndi mtumiki wa wonse." 36 Anathenga kamwana ndikukaika pakati kawo. Anamnyamula pakwanja nati kwa iwo, 37 "Aliyense amene azalandira mwana ngati uyu mzina langa, alandila inenso, ndipo ngati wina alandila ine, sanalandire ine cabe, koma iyenso amene anandituma." 38 Yohane anati kwa iye, "Mphunzisi, tinaona wina alikutulusa ziwanda mzina lanu ndipo tinamulesa iye, cifukwa satisatira ife." 39 Koma Yesu anati, Musawalese iye, cifukwa palibe amene azacita nchito ya mpamvu mzina langa ndi kuyamba kuninyoza pambuyo paka. 40 Aliyense amaene satisusa alinase. 41 Aliyense amene azakupasani kapu ya manzi kuti mumwe cifukwa muli a Kristu, zoonadi ndinena kwa inu, sazathaya mpoto yake. 42 44 Aliyense amene azakumudwisa kamozi ka utu tokhulupirira, cizakhala bwino kwake kutenga cimwala cikulu ndikumumangila naco m'mukosi ndikumuponya mcimana. 43 Ngati zanja lako likukumudwisa, ijuwe. Ciliko bwino iwe kunkangena kumoyo wopanda zanja kupambana kukangena kugehena ndi manja awili kumoto wosazima. 45 Ngati kwendo kwako kwakukumudwisa, kujuwe. Kulibwino kwako kukangena ku moyo wolemala kupambana kuponyewa ku gehena ndi mendo 46 awili. 47 Ngati diso lako yikukumudwisa, icose. kuli bwino kwako kukangena ufumu wa Mulungu ndi diso imozi kupambana kukangena ku gehena ndi menso awili, 48 kwamene kuli vikusi vyamene sivikufa, ndi moto suzima. 49 Cifukwa aliyense azayesedwa ndi moto. 50 Mcele ndiwabwino, koma pamene mcele ukutha kukonda, kodi ungaupange bwanji kuti ukonde nafuti? Nkhalani mcele pakati kanu, ndipo nkhalani m'mtendele wina ndi mzace."