Mutu 7

1 Bafalisi na balembi benangu bamene banachokela ku Yelusalemu banasonkhana pamene anali. 2 Ndipo anaona kuti wophunzila bake benangu banalikudya buledi na manja yodesedwa, yamene yosasamba. 3 (Chifukwa Bafalisi na Mayuda wonse sibanali kudya wosasamba kumanja, chifukwa banagwililila kumwambo wa makolo. 4 Pamene Bafalisi bachokela ku msika, sibanali kudya ngati sibanasambe, na kugwililila ku vinthu vonse vinangu banalandila, monga ku kusuka makapu, mapoto, viya na Tebulo yodyelapo.) 5 Bafalisi na balembi banamufunsa Yesu, " Kodi nichani wophunzila bako sibayenda mumwambo wa makolo, chifukwa bakudya buledi wosasamba kumanja?" 6 Koma anabauza kuti, "Yesaya ananenela bwino pali imwe bachinyengo. Chinalembewa, 'Aba banthu banilemekeza na milomo chabe, koma mitima ili kutali na ine. 7 mapembezo yalibe chilichonse ndiyo banipasa, kuphunzisa malamulo ya banthu monga chipunziso chawo. 8 Munataya malamulo ya Mulungu ndikukonkha miyambo ya banthu." 9 Anabauzanso kuti, "Munachita bwino bwanji pokana malamulo a Mulungu kuti musunge miyambo yanu! 10 Chifukwa Mose anakamba kuti, 'Lemekeza batate bako na bamai bako,' Aliyense wamene akamba voyipa pali batate kapena bamai bake azafa zoona.' 11 Koma mukamba kuti, ' ngati munthu akuti kuli batate bake kapena bamai bake, "Iliyonse thandizo yocokela kwa ine ni Kobani, "kutanthauza kuti, 'yopasiwa kwa Mulungu')- 12 Ndipo simufunika kumuvomeleza munthu uyo kucita chilichonse kuli batate bake kapena bamai bake. 13 mupanga mau ya Mulungu kunkala yalibe mpamvu chifukwa miyambo yanu yamene mupasana. Navinthu volingana vamene muchita." 14 Anaitana gulu yabanthu na kukamba kuti, " mvelani kwa imwe, imwe bonse, na kumvesesa. 15 Kulibe chochokela kunja kwa munthu chingaononge munthu pamene chingena mkati. Koma chamene chichokela mukati mwa munthu ndiye chingamuononge." 16 Yense ali ndi makutu amve 17 Manje pamene Yesu anachoka pa gulu ya banthu na kungena munyumba, wophunzila bake banamufunsa pali fanizo. 18 Yesu anakamba kuti, " Naimwe mukalibe kunkala nachinveseso? Simuona kuti chamene chingena mu munthu kuchokela kunja sichingamuipise munthu, 19 cifukwa siciyenda mkati mwa mtima, koma cimayenda m'mala ndikupita ku ciphuzi?" pali ici Yesu anatanthauza kuti cakudya chili chonse nichoyela. 20 Anakamba kuti, "Ni chija chamene chicokela mukati chamene chiipisa munthu. 21 Chifukwa kuchokela mukati mwa munthu, kuchokela mumutima, muchokela maganizo yoipa, zachiwelewele, zaukawalala, zakupaya, 22 zachigololo, zokumbwa, zoipa, zachinyengo, kuzitukumula, zopusa. 23 Zonse izi zoipa zichokela mukati, ndiye zimene ziipisa munthu." 24 Anaima nakuchoka kuja na kupita kudela ya Tire na Sidoni. Kwamene kuja anayenda munyumba, ndipo sanafune munthu aliwonse kuziba kwamene analili, koma sanakwanise kubisama. 25 Koma pamene mukazi wamene anali na mwana wake mukazi wamene anali na mizimu yonyasa ananvela pali eve, anabwela kuli eve na kugwada pansi pa mendo yake. 26 Mukazi uja anali wa chigiriki, mutundu wa Musurofonika. Anamupempha kuti achose chibanda kuchoka mumwana wake mukazi. 27 Anamuuza kuti, "Leka bana badye choyamba. Chifukwa sichili bwino kutenga buledi ya bana na kuponyela bagalu." 28 Koma anayankha na kuli eve, "Zoona, Ambuye, chikanga ibwa zimadyako vamene vikugwa pa tebulo yamene bana badyelapo." 29 Anamuuza kuti, " Chifukwa cha vamene wakamba, ndiwe womasuka kuyenda. Vibanda vatuluka mu mwana wako mukazi." 30 Anabwelela kunyumba kwake nakupeza mwana wake muzazi aligone pa mpasa, na vibanda nishi vayenda. 31 Ndipo anachoka nafuti kuchoka ku muzinda wa Tire, na kupitilila ku Sidoni ku nyanja ya Galileya kufikila ku malo ya ku Dekapolisi. 32 Ndipo anamuletela munthu winangu wamene sanali kumva ndipo wosalankula, ndipo anamupempa kuti amusanjike manja yake pali eye. 33 Ndipo anamutenga eve pambali kuchoka pa gulu ya banthu,anaika chikumo cake mumakutu yake, na kutunya mata na kugwila lulime lwake, 34 Analangana kumwamba, nakumuuza kuti, "Efefata," kutantauza kuti, "Seguka!" 35 Pantawi yamene iyo matu yanaseguka, ndi camene cinalikugwila lilime lake cinaonongeka ndipo anayamba kulankhula bwino. 36 Ndipo analamulila beve kuti basauze munthu aliyense. Koma mwamene anabauzila maningi, ndiye mwamene banauzila maningi banthu. 37 Banali wodabwa maningi, na kukamba kuti, " Achita vintu vonse bwino. Alengesa na wosanvela kuyamba kunva na wosakamba kuyamba kukamba."