Mutu 13

1 Pamene Yesu anayenda kuchoka mutempele, umodzi wa wophunzila bake anati kwa iye, "Mphunzisi, wonani myala zabwino na zomanga zabwino!" 2 Anamuuza kuti, " Waziona izi zomangidwa bwino? Palibe mwala uliwonse wamene uzasala pamwamba pa unzake wamene siuzachosewapo." 3 Pamene anankhala paluphiri lwa Oliva kumbali kwa tempele, Petulo, Yakobo, Yohane na Anduleya anamufunsa kumbali, 4 "Tiuzyeni, nanga ivi vizachitika liti? Nichani choonesela kuti ivi vinthu vili pafupi nakuchitika?" 5 Yesu anayamba kubauza kuti, "Nkhalani chelu kuti wina asakusobeseni. 6 Bambili bazabwela muzina yanga nakuti, 'Ndine wamene, 'ndipo azasobesa bambili. 7 Koma mukamvela va nkhondo na nkhani za nkhondo, musakavutike mutima, ivi vinthu vifunika kuchitika, koma kusila kwa dziko kukalimbe kucitika. 8 Chifukwa ziko izaukila mosusana na ziko, na ufumu uzaukilana mosusana na ufumu. Kuzankhala chogwendeza ziko mumadela yambili, na njala. Ivi ndivo voyamba va kubaba pobala. 9 Nkalani bachelu. Bazakupelekani kuli bakulu bansaka, ndipo muzakamenyewa mumasunagogi. Muzakaimilila kuli bakulu ba boma na mafumu cifukwa cha ine, ngati umboni kuli beve. 10 Koma uthenga wabwino ufunika kuti ulalikiliwe ku maiko yonse. 11 Pamene bazakakugwilani nakukupelekani, musakachite nkhawa kuti tizakakamba chani. Chifukwa pantawi ija, vamene muzakakamba vizakapasiwa kuli imwe; simuzankala imwe wokamba, koma Muzimu Woyela. 12 Mubale azakapeleka mubale munzake ku infa, ndipo tate azakapeleka mwana wake. Na bana bang'ono bazaukila makolo yawo nakufuna kuti bapaiwe. 13 Bazakuzondani banthu bambili chifukwa cha zina langa. koma wamene azalimbikila kufikila kuchimalizilo, uja munthu azaphulumusiwa. 14 Ndipo mukaona zamalodza zosavomelezewa ziimilila pamene sizifunika kuimiliila," (lekani bamene baziba kubelenga banvesese) "lekani awo bali ku Yudeya batamangile ku maluphili, 15 lekani uyo ali pamwamba pamutenge wa nyumba asaseluke kungena munyumba kapena kuti akatenge chili chonse kuchosa munyumba, 16 ndipo lekani uyo ali mu munda asabwelele kuti athenge chovala chake. 17 Koma soka kuli baja bamene bali na bana mumala na bamene onyosha bana mumasiku yaja! 18 Pemphelani kuti visakachitike muthawi ya mphepo. 19 Chifukwa kuzankhala mazunzo yakulu, yamene yakalibe kuchitikapo kuchoka pachiyambi, pamene Mulungu analenga ziko lapansi, kufikila manje, kulibe, kapena sikuzankhalanso. 20 Kapena Ambuye akachepeseko masiku, kulibe aliyense wamene azaphulumusidwa. Koma chifukwa cha awo wolungama, bamene awo banasankha, azachosako masiku. 21 Koma ngati winangu akuuzani kuti, 'Onani uyu ndiye Kristu!' kapena Onani, kuja ndiye kwamene alili! Musakhulupilile. 22 Chifukwa ba Kristu baboza na baneneli baboza, bazaonekela nakuonesa vizindikilo na vodabwisa kuti baname, ngati nikoteka nakuli awo wolungana. 23 Nkhalani celu! Nakuuzani vonse ivi pamene nthawi ikhaliko. 24 Koma kukasila kusausidwa pamasiku yaja, zuba izasandulika mudima, mwezi suzapelekanso kuwala, 25 nyenyezi zizagwa kucokela kumwamba, ndi mpamvu zamene zili kumwamba zizasung'uzika. 26 Ndipo muzaona Mwana wa Munthu alikubwela mumakumbi ndi mpamvu zikulu na ulemelelo. 27 Ndipo azatuma bangelo bake azasonkhanisa wonse wolungama kuchokela kumbali zonse zili 4, kuchokela kosilila dziko na kosilila kwa thambo. 28 Mphunzilani chiphunziso cha mutengo wa mukuyu. pamene muona misambo iyamba kupukila ndikuyoyosha matepo, muzibe kuti nthawi ya kupya kuli pafupi. 29 Chimozi-mozi pamene muona ivi vichitika, muzibe kuti ali pafupi, pafupi na pakomo. 30 Zoona nikuuzani, uyu mubadwo siuzapita pamene ivi vizachitika. 31 Kumwamba na ziko lapansi zizapita, koma mau yanga siazapita. 32 Koma kulingana za siku kapena nthawi, palibe wamene azaziba, chikanga bangelo kumwamba, kapena Mwana koma Atate. 33 Nkhalani acelu! Yanganani ndi kupemphela cifukwa simuziwa nthawi yamene iyo. 34 Cilingana ndi munthu amane anayenda paulendo- anasiya nyumba yake ndikuikamo anchito kuti akale woyiyanganila, aliyense ndi nchito yake ndipo analemba na woyangana kuti ankhale m'maso. 35 Cifukwa cake nkhalani ndi celu, cifukwa simuziwa pamene mwine nyumba azabwela; kungankale m'mazulo, kapena pakati kausiku, kapena pamene kombwe alikulila m'mamawa, nangu kuseni. 36 Ngati azabwela movundumukiza, asakakupezani muli mtulo. 37 Camene nili kunena ine kwa inu ndilikunena kwali aliyense: Nkhalani maso!"