Mutu 11

1 Manje pamene anabwela ku Yelusalemu, anali kufupi ndi Befifagi ndi Betani, paluphiri lwa Oliva, ndipo Yesu anatuma awiri wophunzira ake 2 ndipo anAti kwa iwo, "Pitani ku munzi wakumbali ina. Pamene mngena mzapenza kamwana ka bulu kamene wina akalibe kukwelapo. Mkamasule ndikubwela nako kwanga. 3 Ndipo ngati wina azanena kwa inu, 'cifukwa cani mulikucita telo?' Mmuwuze, 'Ambuye akafuna ndipo tizakabwe lesa mwamsanga." 4 Ndipo anayenda anampeza mwana wa bulu womanga pongenela kunja kwa njira, ndipo anamumangulula. 5 Ndipo anthu ena anali imirire panja anati kwa iwo, "kodi mulikucita ciani, kumasula kamwana ka bulu?" 6 Anakamba kwa iwo mwamene Yesu anawauzira, ndipo anthu anawalola kuti ayende. 7 Aja awiri wophunzira ake anabwelesa kaja kamwana ka bulu kwa Yesu ndipo anaikapo manyula kuti Yesu akwerepo. 8 Anthu ambiri anayazinkha nyula zawo mnjira, ndi ena anayanzikha misambo ya vimitengo vyamene anatyola kufumila muminda. 9 Aja amene amene anali patsogolo ndi aja amene anali kumbuyo anali fuula nati, "Hosana! Odala ndi iye amene abwela mzina la Ambuye. 10 Odala ndi uyo ufumu wa wa atate athu Davide wamene ubwela! Hosana mumalo wokwezedwa mwamba!" 11 Ndipo Yesu anangena m'Yelusalemu ndikuyenda m'tempele ndi kukaona zonse zamene zinalimo. Manje, nthawi itapita kale, anacoka kuyenda ku Betaniya ndi aja tewlufu. 12 Siku yokonkhapo, pamene anacokela ku Betaniya, anamvela njala. 13 Ndipo anaona patali cimtengo ca mkuyu cinali na matepo, anayenda pafupi kukaona ngati angapezeko cipatso momwemo. koma pamene anafika pafupi, sanapezamo ciliconse koma matepo, cifukwa sinali nyengo yake. 14 Analankhula naco, "Palibe amene azadyamo futi cipatso mwaiwe." Ndipo wophunzira ace anamva izi. 15 Anabwela ku Yelusalemu, ndipo anangena m'tempele ndipo anayamba kucosa aja wogulisa ndi wogula m'tempele. Anagudubula matebulo ya aja wocinja ndalama ndi ponkhala aja wogulisa nkhunda. 16 Sanalole aliyense kuti anyamule ciliconse kucosa m'tempele kuti ciguliwe. 17 Anawaphunzitsa nati, "kodi sivinalembedwe, "Nyumba yanga izacedwa nyumba ya mapemphero ya dziko lonse'? Koma inu mayipanga kunkhala nyumba ya Kawalala." 18 Akulu ansembe ndi alembi anamva zimene analankhula, ndipo anafuna-funa njira yompayilamo. Anali ndi mantha cifukwa annthu wonse anacitha cidwi ndi ciphunzitso cake. 19 Ndipo nthawi zonse kukafika mazulo, anthu anali kucoka m'muzinda. 20 Pamene analikuyenda m'mawa mwake, anaona uja mtengo wa nkhuyu wauma kucokela ku mizyu. 21 Petulo anakumbuka nati, "Rabbi, Onani! Cija cimutengo ca mkhuyu camene munatembelela cauma conse." 22 Yesu anayankha nati, " Nkhalani ndi cikhulupiriro mwa Mulungu. 23 Zoonadi ndikuwuzani kuti aliyense amene azalankhula ku phiri iyi,' ndipo sakaika m'mtima wake koma akhulupirira kuti zamene walankhula zizacitika, ndiye camene Mulungu azacita. 24 Ndiye cifukwa cake ndilankhula nanu: Ciliconse camene mzapemphelelapo ndi kupempha , khulupirirani kuti mwacilandila, ndipo cizankhala canu. 25 Nthawi zonse pamene muimirira ndi kupemphera, mufunika kukululukira aliyense amene anakucimwilani, kuti Atatet alikumwamba akukululukireni inutso macimo yanu." 26 koma ngati simukhululukira ena , Atate akumwamba sazakukululukirani nainutsu. 27 Anabwelelatso ku Yelusalemu. Pamene Yesu anali kuyenda m'tempele, Akulu ansembe, ndi alembi ndi akulu anaza kwa iye. 28 Anati kwa iye, "Kodi usewenzesha ulamuliro wotani pa ivi vonse? Ndipo ndindani amene anakupatsa ulamuliro wocita ivi? 29 Yesu anati kwa iwo, " Naine ndizakufunsani funso imozi. Ndiuzeni ine ndipo ndizakuwuzani pa ulamuliro wamene ndicitilamo ivi. 30 Kodi ubatizo wa Yohane, unali wocokela kumwamba kapena ku Anthu? Niyankheni." 31 Anakhambilana pakati kawo ndikususana nati, "ngati tizati, 'kucokela kumwamba,' iye azati, 'cifukwa nicani simunamkhulupirire?' 32 Koma tikati, 'kufumira ku anthu,'..." analikuyopa anthu, cifukwa anthu wonse anazindikira kuti Yohane anali mneneri. 33 Ndipo anamuyankha Yesu nati, "Sitiziwa." Ndipo Yesu anati kwa, "Nainetso sindizakuuzani pa ulamuliro wamene nicitila izi."