Chapita 2

1 Pamenepo Yoswa mwana wa Nuni mwacisinsi anatuma amuna abili kutuluka mu sitimu monga ozonda. Ana kamba, ''Yendani, Tanganani paziko, makamaka Teriko.'' Iwo anayenda na kufika panyumba ya hule wina zina yake anali Rahabi, nakupona mwamwene. 2 Zinauziwa kuli mfumu yako yeliko, ''ona, bamuna ba ku Israyeli abela kuna kuza zonda (spy) ziko malo.'' 3 Mfumu yako Jeriko inatuma mau kuli Rahabi na kukamba kuti, '' cosa bamuna babwela kuli iwe amene anangena mu nyumba yako, cifukwa ba bwela kuzazonda muziko yonse.'' 4 Koma muzimai anatenga bamuna awili nakuba bisa. Anayankha,'' bamuna banabwela kuli ine, koma sini na ziba kwa mene banacoka. 5 Banayenda pamene kwenze kofipa, pamene yenze nthawi yovala ciseko ca mu mzinda. Siniziba kwamene bayenda muza bagwira ngati mwaba konka msanga.'' 6 Koma anabakwelesa pamwamba pamalata na kubabisa namitenga yamene anaika pamalata. 7 Ndipo bamuna anaba pepeka pa njira yopita ku Yolodani. Ciseko cinavalika pamene opepeka anacoka. 8 Bamuna banali basanapone usike, pamene iye anakwela pamalata. 9 Anakamba kuti,'' niziba kuti Yehova akupasani malo na mantha yoyopa imwe yabwela pali ife. Onse bamene bakhala muziko baza sungunuka pamenso yako. 10 Tinamvela mwamene Yehova anayumisila manzi ya mu nyanja imwe pamene pamene munacoka ku Eigipito. Tinamvelanso vamene munacita kumafumu yabili yaku Amori kumbali ya Yolodani - sihoni na ogi - yamene munabonongelatu. 11 Mwamusanga pamene tinamvela mitima yathu yanasungunuka kunalibe na mphavu inasala muli ali bonse - popeza Yehova mulungu wanu, nimulungu wa mwamba kumwamba na paziko ya pansi. 12 Manje apa, lumbilani kwa ine zina ya Yehova kuti, mwamene nakhalila nacifundo naimwe, naimwe muzakhalanso nacifundo nanyumba ya batate wanga. Nipaseni cizindikilo ca zoona. 13 Kuti muzasunga mayo wa batate banga, bamai binga, abale, alongo banga namabanja yaba yonse, nakuti uzatipulumusa ku imfa.'' 14 Bamuna banakamba kuli yeve,'' moyo wathu na moyo wanu, ingakuale ku imfa! ngati suzakamba vamene tabwelela, manje pamene Yehova azatipasa malo aya tizakhala nacifundo na ku khulupilika kwa iwe.'' 15 Pamene anaba seiusa na nthambo kupitila pa windo. Nyumba mwamene benze kukhala inama ngiwa mulinga ya mumzinda. 16 Anakamba kwa kuli beve,'' yendani kumapili na kubisama olo okonka angakupezeni. Bisamani masiku yatatu paka okonka bakabwelele. Pamene apo yendani ulendo wanu.'' 17 Bamuna banakamba kuli yeve,'' sitizakhala omangiwa na lonjezu ya lumbilo yamene tinalumbila kuli iwe, Ngati suzacita ici. 18 Pamene tikabwela muziko, ufunika kumanga nthambo yo fiila pawindo pamene watiselusila, na kuika munyumba yako pamozi batate bako na bamai bako ba bale bakona onse ba munyumba ya batate bako. 19 Alibonse wacoka pa khomo ya nyumba yako kupita munjira, magazi yabo yazakhala pamitu yabo ndipo tizakhala tilibe mulandu. koma ngati kwanja kwa ikiwa pali alibonse ali naiwe munyumba, magazi yeke yazakhala pamutupako. 20 Koma ukakamba pali ife, tizamasuka kuli lumbilo unatilapisa.'' 21 Rahabi anayankha, ''lekani yamene mukamba vicitike.'' Anababuza bayenda ndipo banayenda pamenepo amanga nthambo yo fiila mu windo. 22 Banacoka na kuyenda mumapili nakunkhala kuja masiku yatatu paka okonka bana bwelela. Okonka banasakila munjila yonse koma kulibe camene banapeza. 23 Bamuna babili banabwelela nakutauka nakubwela kuli Yoswa mwana wa Nuni, na kumu vza vonse vamene vinacitika kuli beve. 24 Bana kamba kuli Yoswa, ''Zoona Yehova apasa malo aya kuli ise. Bonse banthu bokhala muziko basungunuka cifukwa chaise.''