MUTU 8

1 Bilidati waku shuhiti anayanka nakumba kuti, 2 ''Uzatenga ntawi itali bwanji kukamba vintu ivi? Kufikila liti mawu amukamwa mwako ankhala mpepo yolimba? 3 Kodi mulungu amasokoneza chiweluzo? Kodi wapanvu zonse amasokoneza chilungamo? 4 Bana bako bachimwila eve; tiziba ichi, pakuti anabafaka mumanja ya machimo yawo. 5 Koma tiyerekeze kuti anayesesa kusakila mulungu na kupeleka pempo yako kuli wampanvu zonse. 6 Ngati ndiwe woyere na kuwongoka, mwaicho zoona azazikuza mumalo mwako naku kubweza ku malo yako yoyenera. 7 Ngakale chayimbi chako chinali chaching'ono, mwamene vintu vilili unkalidwe wako wosilizila uzankala ukulu maningi. 8 Napapata funsa mibadwe wakudala, nakuonesa kuli vamene makolo batu banapunzila. 9 ( Tinabadwa chabe mailo ndipo sitiziba vilivonse chifukwa masiku yatu pa ziko ya pansi yali ngati mtunzi.) 10 Sibazakupunzisa nakukuuza? sibazakamba mau kuchokela mumitima yao? 11 Kodi mutengo wa gumbwa ungakule kulibe dabwa? Kodi mateya yanga kule kulibe manzi? 12 Pamene yakali gilini na kutemewa, yamafota vomela vinangu vikalibe. 13 15 Ndiye mwamene zilili njila za bonse bamene bamaibala mulungu; chiyembekezo cha balibe mulungu chizakafa. 14 Chidalilo chake chizayabanika, na chikulupililo chake chizafoka monga kangaude. Amasamila pa nyumba yake, koma sizamutandiza; amayigwilila, koma siyima imilila. 16 Pansi pa kazuba ali gilini na, mpukila zake zima yenda mu munda wake onse. 17 Mizyu zake nizomangiwa mozungulukila milu ya myala; imasakila malo yabwino pakati pa myala. 18 Koma ngati muntu uyu awonongeka kuchokela mumalo yake, mwicho malo yaja yazamukana nakukamba kuti, 'nikalibe kukwonapo iwe.' 19 Ona, ichi ndiye ''chisangalalo'' cha machitidwe ya muntu waso; mbewu zina zizatuluka muntaka ya mumalo yake. 20 Ona, mulungu sazapisha muntu alibe mulandu; kapena kugwila kwanja kwa muntu wochita voipa. 21 Azazulisa kamwa yako nakuseka, milomo yako na kupunda. 22 Abo bamene bakuzonda bazavalikiwa na manyanzi; hema ya bantu boipa sizankalapo futi.''