MUTU 4

1 Ndipo Elifazi waku temaniti anayanka nakukamba kuti, 2 ngati aliyense ayese kukamba naiwe, ungankale osa nkazika mutima pansi? Koma nindani angazilese kukamba? 3 Ona, walangiza bambili; walimbisa manja yofoka. 4 Mau yako yanatandiza wamene anali kugwa; unapanga magufi yofoka kulimba. 5 Koma manje vwuto yabwela kuli iwe, ndipo ndiwe otopa; ndipo ndiwe ovutika. 6 Kodi manta yako si chidalilo chako, na kunkazikika kwa njila zako chiyembekezo chako? 7 Ganizila pali ivi, napatata: Nindani anaonongeka osalakwa? 8 Kapena niliti pamene bantu bo wongoka bana jubiwapo? Kulinganya na vamene naona, bamene bamalima voipa nakushanga mavwuto bama kolola vamene. 9 Nakupema kwa mulungu banawonongeka; naku polika kwa ukali wake banm dyewa. 10 Ku uwula kwa mukango, mau ya mukango woyofya, meno ya mikango ing'ono- amatyoka. 11 Mikango yokota imafa chifukwa cho soba bo vutisa; bana ba mkango ikazi bama mwazikana paliponse. 12 Manje nkani inangu inabwelesewa kuli ine mobisa, ndipo matu yanga yanalandila kumgongoza kwa yeve. 13 Ndipo kunabwela maganizo kuchokela ku mensophenya ya usiku, pamene tulo tukulutuma gwela pa bantu. 14 Kunali usiku pamen manta nakunjenjema kunabwela pali ine, ndipo mabonzo yanga yonse yana nyang'ana. 15 Muzimu anapita pa menso panga, na sisi yapatupi panga inanyamuka. 16 Muzimu wanga unayimilila, koma sinina zindikile mawonekedwe yake.Mawonekedwe yanali pa menso panga; kunalibe chongo, ndipo ninanvela mau yamene yanakamba kuti, 17 ''Kodi muntu tupi akwanisa kunkala olungama kuchila mulungu? Kodi muntu angamkale oyela kuchila wamene anamupanga? 18 Ona, ngati mulungu samaika chikulupililo muli banchito bake; ngati aimbila mulandu bangelo bake vopusa, 19 chingankale bwanji kuli bantu bamene bankala munyumba ya madoti, bamene miziko yao yali mufumbi, bamene bama shanyauka musanga kuchila njenjete? 20 Pakati pa kuseni na mumazulu bama onongeka; bana onongeka muyayaya kulibe aliense wakubzindikila. 21 Kodi zingwe za mahema yao sizidulidwa pakati pawo? Bamafa; bamafa ninshi kulibe nzelu.