1 Aya ndiye mau ya Yeremiya mwana wa Hilikiya, umozi wa ansembe a ku Anathothi muziko ya Benjamini. 2 Mau ya Yehova yanabwela kuli iye mumasiku ya Yosiya mwana wa Amoni, mfumu ya Yuda, muchaka chakhumi na chitatu cha ulamulilo wake. 3 Inabwela futi mumasiku ya Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, mpaka mwezi wachisanu wa chaka chakhumi na chimozi cha ulamulilo wa Zedekiya mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, pamene banthu ba ku Yerusalemu anatengewa kupita ku ukapolo. 4 Mau ya Yehova yanabwela kuli ine, kuti, 5 ''Pamene nikalibe kukupanga iwe mumimba, ninakusankha ; ukalibe kutuluka mumimba, ninakupatula iwe; Nina kupanga muneneli muziko yonse.'' 6 “Aa, Ambuye Yehova!'' Ninakamba kuti, “Siniziba kukamba, pakuti ndine wamungono kwambili.'' 7 Koma Yehova anakamba kuli ine, '' Usanene, Ndine wamungono.'' Uyende kulikonse kwamene nizakutuma ndipo ukakambe chilichonse chamene nizakulamula ! 8 Usabayope, pakuti nili na iwe kuti nikupulumuse - Ndiye kukambilila ya Yehova.'' 9 Pameneapo Yehova anamasula kwanja wake, na kukata pakamwa panga, nakukamba kuti, 10 Manje nayika mau yanga mukamwa mwako. nikuika lelo pa mitundu ya banthu na pa maufumu, kuzula, kugwesa, kuwononga na kupasula , kumanga na kushanga.” 11 Mau ya Yehova yanabwela kwa ine, kuti, “Kodi wuona chani, Yeremiya?'' Inayanka kuti, “ Naona nthambi ya amondi.'' 12 Yehova anakamba kwa ine, ''Waona bwino, pakuti niona mau yanga kuti yachitike.'' 13 Mau ya Yehova anabwela kwa ine kachibili, kuti, ''Uona chani?'' Ine ndinati, “Naona mphika wotentha, yamene nkhope yake ikunjenjemela, kuchokela kumpoto.'' 14 Yehova ananiuza kuti, ‘'Soka izagwela banthu bonse onkhala muziko lino kuchokela kumpoto. 15 Pakuti niyitana mafuko yonse ya maufumu ya kumpoto- ndiye kukambilila kwa Yehova. Azabwela, ndipo aliyense azaika mupando wake wachifumu pachipata cha zipata za Yerusalemu, malinga na makoma yonse ozungulila mu muzinda, na yonse mizinda ya Yuda. 16 Nizabaweluza chifukwa cha zoipa zawo zonse pakunisiya Ine, kuchoka nsembe kwa milungu ina, na kulambila zamene anapanga na manja yawo. 17 Dzikonzekeretseni! Imirira ndi kunena kwa iwo chirichonse chimene ndikulamulira iwe. Usatyoledwe pamaso pawo, kuti ndingakuphwanye pamaso pawo. 18 Taonani! Lero ndakusandutsa mzinda wokhala ndi mipanda yolimba kwambiri, mzati wachitsulo ndi makoma amkuwa pomenyana ndi dziko lonse pa mafumu a Yuda, akalonga ake, ansembe ake ndi anthu a m’dzikolo. 19 Iwo adzamenyana nawe koma sadzakugonjetsa, chifukwa ine ndidzakhala ndi iwe kuti ndikupulumutse, watero Yehova.”