Mutu 61

1 Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine, chifukwa Yehova wandidzoza ine ndilalikire mawu abwino kwa ozunzika. Adanditumiza kuti ndikachiritse osweka mtima, ndikalalikire za amasulidwe kwa andende, ndikutsegulira ndende kwa iwo omangidwa. 2 Ananditumiza ndikalalikire chaka chokomera Yehova, tsiku lobwezera la Mulungu wathu, ndi kutonthoza onse amene akumva chisoni. 3 Wandituma, kuti ndipatse iwo akulira m'Ziyoni, kuti ndiwapatse nduwira m'malo mwa phulusa, ndi mafuta achimwemwe m'malo mwa maliro, ndi chovala chomtamanda m'malo mwa mzimu wofatsa, ndi kuwatcha mitengo ya chilungamo, kubzala kwa Yehova, kuti alemekezedwe. 4 Iwo adzamanganso mabwinja akale; adzabwezeretsa malo akale amene anali kuwonongedwa kale. Iwo adzabwezeretsa mizinda yopasuka, mabwinja a mibadwo yambiri yakale. 5 Alendo adzaimirira ndi kudyetsa zoweta zanu, ndipo ana a mlendo adzalima minda yanu ndi minda yamphesa. 6 Mudzatchedwa ansembe a Yehova; adzakutcha atumiki a Mulungu wathu. Mudzadya chuma cha amitundu, mudzadzitamandira chifukwa cha chuma chawo. 7 M'malo mwa manyazi anu mudzalandira kawiri; ndipo m'malo mwamanyazi adzakondwera ndi gawo lawo. Choncho adzalandira magawo awiri a dziko lawo; adzakhala ndi chimwemwe chosatha. 8 Pakuti ine Yehova ndimakonda chilungamo, ndipo ndimadana ndi zauchifwamba ndi chiwawa chosachita chilungamo. Ndidzawabwezera mokhulupirika, ndipo ndidzapangana nawo pangano losatha. 9 Mbadwa zawo zidzadziwika pakati pa anthu a mitundu ina, ndi ana awo pakati pa anthu. Onse amene adzawaona adzawazindikira, kuti ndiwo anthu amene Yehova wawadalitsa. 10 Ndidzakondwera mwa Yehova; mwa Mulungu wanga ndidzakondwera. Pakuti wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso; wandiveka ine ndi mwinjiro wachilungamo, monga mkwati amadziveka nduwira, ndiponso monga mkwatibwi azikometsera ndi zibangiri zake. 11 Pakuti monga dziko lapansi limeretsa zipatso zake, ndi m'munda momwe umalimamo, momwemonso Ambuye Yehova adzaphukitsa chilungamo ndi chiyamiko pamaso pa amitundu onse.