Mutu 49

1 Nvela kuli ine, iwe kumbali kwa manzi! manje niveseni, imwe bantu bakutali. Yehova aniitana ine nazina yanga kuchokela pamene nina banda, pamene ba mayi banga bana ni bwelesa mu ziko. 2 Anapanga kamwa kanga monga lupanga lakutwa, anani bisa ine muchivwili vwili cha manja ake; anani panga mivwi yo pangedwa bwino; mu mutuzi wake anibisa ine. 3 Anakamba kuli ine, ''iwe ndiwe wanchito wanga, israeli, mwamene nilangiza ulemelelo wanga.'' 4 Koma nina yanka, ''ngakale nina ganiza kuti nagwila nchito mwachabe, naononga mphavu yanga pa chabe, koma kuweluza kwanga kuli muli Yehova, namalipilo yanga ali kuli mulungu.'' 5 Manje Yehova anakamba -wamene ananiumba ine nikalibe ku badwa kuti mikankale wanchito wake, kubwezela Yakobo futi kuli eve kwakuti israeli akasokanisiwa kuli eve, chifukwa ndine wolemekezewa pa menso pa Yehova, ndipo mulungu ankala mphavu yanga - 6 ndipo akamba, ''nikuti kang'ono kuti iwe unkale wanchito wanga kuti ukazikise mutundu ya Yakobo, na kubwezela opulumuka a israeli.Niza ku panga nyali ya bantu ba mitundu kuti unkale chipulumuso changa paka kusilizila kwa ziko.'' 7 Ichi ndiye chamene Yehova akamba, muomboli wa israeli, woyela wao, kuli uyo wamene umoyo wake niwo suliwa, ku zondewa na maiko, ndipo kapolo wa olamulila, ''mafumu azakuonani nakunyamuka, na bana bafumu bazakuonani naku gwada pansi, chifukwa cha yehova wokulupilika, ngakale woyela wa israeli, wamene anakusanka iwe.'' 8 Ichi ndiye chamene Yehova akamba kuti, pa ntawi yamene naganizila kukulangiza chisomo niza kuyanka iwe,ndipo pa siku lachipulumusoniza kutandiza iwe; niza kuchingiliza iwe na kukupasa unkale pangano la bantu, kumanga malo, kubwezela malo osiiwa malo olobelela. 9 Uzakamba kuli bomangidwa, 'chokani panja;' kuli abo bali mumigodi wofipa, 'zilangizeni inwe mweka.' Bazadyela mumbali mwamanjila, naku mutetemuka kulibe chilichonse kuzankala kodyela mauzu. 10 Sibazanvela njala olo njota; kapena kupya olo zuba sikuza fika pali beve, pakuti iye ali nachifundo pali beve azba sogolela beve; azabalangiza beve kumusinje ya manzi. 11 Mwaicho niza panga mapili kunkala manjila, naku panga njila zitali kulinganiza.'' 12 Onani, ichi chizabwela kuchokela kutali, vinangu kuchoka kumpoto na kumazulo; navinangu kuchoka ku malo a sinimu. 13 Imbani, kumwamba, na kusangala, ziko lapansi; mupwanyike mumaimbidwa, imwe mapili! pakuti Yehova atotoza bantu bake ndipo amanvela chisoni kuli bovutisiwa. 14 Koma ziyoni anakamba kuti, '' Yehova anisiya ine ndipo ambuye aniibala ine,'' 15 ''Kodi muyi angayibale mwana wake, amene anyonka, osanvela chisoni kuli mwana wamene anabala eka? Inde, bangaibale, koma ine sinizakuibala iwe. 16 Onani, nakulemala zina yako pamanja yanga; vipupozako vili pasogolo panga. 17 Bana bako babwela moyendesa, abo bamene banali kukuonanga bayenda. 18 Yangana mozuguluka nakuona, bonse bakusokana ku bwela kuli iwe. Pamene nikali na moyo -uku ndiye kukambila kwa Yehova - uzaba vala aba monga mabanga na kubafaka aba monga mukazi wofuna kukwatiliwa. 19 Ngakale munali zinyalala nakuchepekela, malo amene anali wonongeka, apo manje muzankala bang'ono mu malo yonkalapo, na bamene bana kuongani bazankala kutali. 20 Bana bobadwa ntawi yamalilo yanu bazakamba mukunvela kwanu, 'malo niya ng'ono kuli ise tipezeleni malo, kuti tinkale kuno.' 21 Ndipo uza zifunsa iwe weka, 'nindani wamene anibalila aba bana ine? ninali wofelewa ndipo ngomwa, wotengewa ukapolo na kupishiwa kuchikwati. Nindani abakulisaaba bana? Onani, nenzeninasiiwa neka nanga ichi chachoka kuti?''' 22 Ichi ndiye chamene ambuye Yehova akamba kuti, ''onani, nizanyamula kwanja yanga ku maiko; niza nyamula ndembela yachilangizo kuli bantu. Bazabwelesa bana bako bamuna mumanja nakunyamula bana bakazi bako muma mpewa. 23 Mafumu azankala abambo alelo ako, nabakazi bamafumu iwe na khope yoyangana pansi nakumyanguta kakungu kaku mendo kwako; ndipo uzaziba kuti ndine yehova; abo bamene bayembekeza pali ine sibaza vesewa manyazi.'' 24 Nanga chuma chingatengewe kuchokela kuli musilikali, kapena ogwiliwa kumasuliwa kuchokela kumukali? 25 Koma icho ndiye chamene Yehova akamba kuti, ''inde, bakapolo bazatengewa kuchoka kuli musilikali, na chuma chizapulumusiwa; pakuti nizalimbana nabo badani banu na kupulumusa bana banu. 26 NIzadyesa okupondelezani nama nyama zao; ndipo bazakolewa namagazi yaobeka, monga ngati amwa vinyu. Ndipo mitundu zonse zizaziba kuti ine, Yehova, ndine mupulumusi wako ndipo wauombola, wa mphavu wa Yakobo.''