Mutu 11

1 Manje chikhulupililo nikunkhala wa simikizila pa vinthu vamene muyembekeza, zosaoneka. 2 Chifukwa ca ici makolo batu anakhala ba chikulupililo. 3 Mwa chikulupililo timvesesa kuti chalo china lengewa na wamu Mulungu mo lamulila, kuti manje vo oneka vinapangiwa mopanda zoneka. 4 Mwa chikulupililo Abeli anapeleka kwa Mulungu nsembe ya bwino yoposa ya Kain, mwa ici anapezeka wolungama ndipo Mulungu anakamba bwino za eve chifukwa cha vopeleka vake, mwa chikulupililo Abeli akamba, ngakhale kuti anafa. 5 Ndi mwa chikulupililo kuti Enoki anatengewa kumwamba kuti asaone infa. " Akalibe kutengewa ku mwamba anachitila umboni kuti anakondwelesa Mulungu. 6 Manje mopanda chikulupililo na chovuta, kukondwelesa, ise. Chifukwa ca ici cho chofunikila kuti aliyense amene abwela kwa Mulungu akhale na chikulupililo kuti aliko kuti ni eve apasa mpaso kwa eve amene amusakila. 7 Ndi mwa chikulupililo kuti Nowa, ngakhale kuti anali anapasiwa mau a Mulungu pa vinthu vosaoneka, na pocita mantha, ya Mulungu apanga combo kupulumba abanja yake. Pakuti ici azudzula ziko lapansi anakhala mwana wa chikulupililo. 8 ndi chikulupililo kuti Abuham, pamene anayitaniwa, anamvelela napita kunja kwa mene anali ku pasiwa vinthu cholowa. Anayenda kunja, osaziba kumene anati apite. 9 Ndi mwa chikulupililo kuti anakhala mdziko ionjezewa imene sinali ya kwao. Anakhala mu msasa na Isaki na Yokobo, Abale ana achiyembe chimodzi. 10 Pakuti analikuyembekezela kuona mdzinda wamaziko opanga naku mangiwa na Mulungu. 11 Mwa chikhulupililo - Sara eve anali cumba- analandila mphamvu nakukhala na mimba ina pitapita nthawi yobala, chifukwa ana khupilila eve amene anamilonjeza. 12 Manje, cokela munthu amene uyu ali pafupi kufa, anabadwa ambili ngati nyenyezi mu mtambo zosawelengeka monga ni muchanga. Mumbali mwa mangi mana. 13 Chinali mwa chikulupililo onse anafa osalandila cilonjezo. Malo mwake ata waona patali nawapasa moni patali, anavomela kuti anali alendo ndi obisama pa ziko lapansi. 14 Pakuti banthu amene akamba mau yaso afuna malo ponkhala. 15 Ngati aganiza za ziko yamene banayendako, anakankhala na mpata wobwelelamo. 16 Koma mene zili, afuna ziko yabwino, kuti ichi, chifukwa ichi, nicha ku mwamba. Mulungu alibe manyazi kuchedwa Mulungu wao, pakuti apanga mzinda waiwo. 17 Chinali mwa chikulupililo kuti Abuham, anayesewa, anapeleka Isake, anali mwana wake mwana eka amene anapeleka, eve, amene analandila eve amene monga mwa molonjezo. 18 Kwa Abuham cinali cinakambiwa, " Nikuchokela kwa Isake kuti mbadwe uzayitaniwa." 19 Abulaham anaganiza kuti Mulungu akwanisa kuusa Isake kuchokela ku infa, kukamba moyelekeza, kunali kwa beve analandila. 20 Chinali mwa chikulupililo mwa vinthu vobwela kwa Isake adalisa Yakobo na Esau. 21 Ndi mwa chikulupililo kuti Yakobo, pamene ali kufa, adalisa onse ana amuna a Yosephe. Yakobo anapempeza, akupunzila pamwamba pa vinthu vake. 22 Mwa chikulupililo kuti Yosephe, pamene analipafu kufa ana kamba pa kucoka kwake kwa ana Isreal ku Egpito , ndipo anawauza zocita pa mafupa yake. 23 Mwa chikulupililo kuti Mose, pamene anabadwa, anabisiwa kwa miyezi itatu ndi makolo ake cifukwa anona kuti anali mwana okongola kwambili.Sanaope Mfumu ulandililo wake. 24 Mwa chikulupililo Mose, pamene akula anakana kuitaniwa mwana wa mkazi wa falao. 25 Anasankha kubvutisiwa ndi anthu ake a Mulungu koposa ku kondwela na mkondwelesa za ucimo kwa ka nthawi. 26 Ana ganiza kuti kubvesewa nsoni paza Kristu kuli kopambana cuma koposa cuma za mu Egipito. Anaika maso pa mpaso yake. 27 Ndi mwa chikulupililo Mose anacoka ku Egipito. Sanaone ukali wa Mfumu, analimbikila monga ngati ali atamuona amene osaoneka. 28 Ndi mwa chikulupililo kuti anasunga pasika nakuwaza kwa magazi, kuti kuononga kwa ana oyamba kusakhuze ana aesilachi oyamba. 29 Mwa chikulupililo anapita pa manzi pa nyanja yamatete monga ngati pambali po yuma. Pamene a Egipito anayesa kucita izi, anamila mu manzio. 30 Ndi mwa chikulupililo kuti chipupa ca Jeriko chinagwa, Athama kuizunguluka masiku asani ndi awili. 31 Ndi mwa chikulupililo kuti Rahabu ule sanafe ndi banja osamvelela chifukwa ana landilila anthu ozonda mzinda mwa mtendele. 32 Nanga nivichani ningakambe apa, pakuti nthawi sindilola ngati ningakambe za Gedioni,Barak, Samson, Jefitali,Davidi, Samuel ndiponso kunena pa aza aneneri. 33 Zinali mwa chikulupililo anali agonjesa maufumu, anacita ku lungamo, ndipo analandila malonjezo. Analekesa pakamwa pa mkango, 34 a zimya mphamvu ya mulilo, bataba kunolakwa lupanga, anacilisiwa ku matenda yonse, anankhala amphamvu mu nkondo, ana gonjeza adani alendo ankhondo. 35 Azimai analandila ba kufa kupitila mu ciukiso. 36 Ena ana menyewa,osalandila kumasuka, kuti amilile mphamvu ya ociukiso yabwino, kumangikwa naku ponyewa mndende. 37 Ena ponyewa miala. anadulilwa pa wili. Anapayiwa nalupanga. Anayenda mu vikumba va nkhosa na mbuzi. Anali anthu ofuma fuma, ndiku nzunzika, anabvutisiwa. 38 Dziko silinali ya bwino kwa eve. Anali kuyenda-yenda mu chipululu namu mapili,godi namu mgodi. 39 Ngankhale kuti anthu awa anali ovomelekezewa na Mulungu chifukwa cha chikulupililo, sana landile lonjezo. 40 Mulungu anakonzelatu za bwino za ise, kuti kulibe ise, ziko ife sizizakhala zo fikapo.