Genesis 18
1
Yehova anaonekela kwa Abraham pa mtengo wa Mamre, pamene anankhala pa ciseko pa kazuba ka siku.
2
Anayanga kumwamba ndipo, onani anaona bamuna batatu baimilila pasogolo pake. Pamene anabaona, anathamanga kukumana noa kucoka pongenela pa nyumba na kugwanda kuika mu wake pansi.
3
Anati, "Ambuye banga, ngati napeza mwai mumenso mwanu, napapata musapitilire wanchito wanu."
4
Lekani manzi yang'ono yabwekesewe, sambani kumendo, pumulani pansi pa mtengo.
5
Lekani nibwelese cakudya cing'ono, kuti muzipumulise imwe mweka. Kucoka apo mungayende, pakuti mwabwelela kwa wanchito wanu. " Bananyankha." Cita monga mwamene wakambila.
6
Ndipo Abrahamu Anayenda kuli Sara mofulumila, naku muuza kuti, "Endesa, tenga mapimo yatatu ya fulaulo, panga fulawa, upange buledi."
7
Pamene apo Abrahamu anatamanga kuyenda ku ng'ombe, nakutenga kang'ombe kamwana kamene kanali kabwino, nakumupasa wanchito, wamene anaenda kukakonza chakudya.
8
Eve anatenga mafuta yonunkira na mukaka, na kamwana kang'ombe kamene kanali kanakonzewa, nakuyika chakudya pasogolo pabo, ndipo anayimirira pafupi nawo pansi pa mtengo pomene beve banali kudya.
9
Ana mufunsa kuti, "Nanga Sara mukaziwako alikuti?" Anayanka kuti, "Ali muja, muhema."
10
Ndipo anakamba kuti, Nizabwera kuli iwe nthawi yamasika, ndipo onani, Sara mukazi wako azakankala na mwana mwamuna. Sara apo anali kumvelera pakomo ya hema yamene inali kumbuyo kwake.
11
Manje Abulahamu na Sara banali banakalamba ndipo banali na zaka zobadwa zambili, na Sara anali atapitirira msinkhu wobala bana.
12
Ndipo Sara anaseka m'mtima mwake, nakukamba mumtima mwake kuti, Pamene nankala nkalamba ine nika pezemo kusangalala?"
13
Yehova anakamba kuli Abrahamu kuti, Nanga nichifukwa chani Sara aseka nakukamba kuti, Nanga nizankala na mwana pamene nakalamba?
14
Nanga kuli chamene akangiwa Yehova? Ntawi ngati yamene ino chaka chamene chibwela Sara azankala na mwana mwamuna."
15
Koma Sara anakana, kukamba kuti, Sininasekeko ine, chifukwa anayopa. Eve anamuyanka kuti, "Iyi, iwe wenze waseka."
16
Pamene apo bamuna baja bananyamuka kuti bayende moyang’ana Sodomu. Abrahamu adaenda nabo kukabapelekeza munjira.
17
Koma Yehova anakamba kuti, "Kansi nimubise Abrahamu chamene nifuna kuchita,
18
po ona kuti Abrahamu azankala mtundu ukulu wamphamvu, ndipo mitundu yonse zapa ziko yapansi zizadalisika muli eve?
19
Pakuti ninamusanka kuti alangize bana bake, na banja yake ya kumbuyo kwake, kuti basunge njila ya Yehova, kuchita chilungamo na chiweruzo, kuti Yehova afikilize kwa Abrahamu vamene anakamba na eve.
20
Pamene apo Yehova anakamba kuti, "Chifukwa chakuti kulira kwa Sodomu na Gomora nikukulu, ndipo chifukwa chimo yawo niyayi kulu maningi,
21
nizaselukila kwamene kuja, kuti nikazionele kulila koshushana nayeve kwamene kwabwela kuli ine, ngati nimwamene mwachitikila. Ngati simwamene, nizaziba. "
22
Pamene apo bamuna baja banapindamuka kucokela kwamene kuja, nakuyenda ku Sodomu, koma
23
Abulahamu anasala ali imilile pamanso pa Yehova. Abrahamu ana fendela pafupi nakukamba kuti, "Manje muzawononga bolungama pamodzi na bantu boipa?
24
Kapena balimo bolungama makumi yasanu mukati mwa mzinda wamene uyu. Nanga muzai ononga yonse, mosayasiya malo aya chifukwa cha bolungama bali makumi yasanu bamene bali mwamene muja?
25
Chinkale kutalitali naimwe kuti muchite chamene ichi, kupaya bolungama pamozi na boipa, kuti bolungama nabeve bachiwe munjila imozi. Chinkale kutalitali na imwe! Nanga muweruzi wa ziko yonse yapansi sazachita cholungama?"
26
Yehova anakamba kuti," Nikapezamo m'Sodomu bolungama makumi yasanu mukati mwa munzi, nizayasunga malo aya chifukwa chao. "
27
Abrahamu anayankha nakukamba kuti, "Onani, nachitenga pali ine kukamba naba Ambuye banga, ngakale kuti ndine doti na milota.
28
Manje ngati kuzakala chabe bolungama bosakwanila makumi yasanu? Nanga muzawononga muzinda wonse chifukwa cha kupelebela bantu basanu?" Anamuyanka kukamba kuti, "Sininga yese kuwu wononga nikapezako makumi yanayi na yasanu."
29
Ndipo anakamba nafuti kuli eve kuti, Nanga bakapezekamo chabe makumi yanayi mwamene muja? Eve anamuyanka kuti, "Sinizachita chifukwa cha makumi yanayi yamene ayo."
30
Ndipo anakamba kuti, Musakalipe, Ambuye, kuti ine nikambe. Nanga mukapezeka chabe kuti muli bali makumi yatatu mwamene muja." Eve anamuyanka kuti, "Sinizachichita, nikapeza makumi yatatu mwamene muja."
31
Ndipo anakamba kuti, Onani, nakamba ba ba Mbuye banga! Manje kapena mwapezeka makumi yabiri mwamene muja. Eve anayanka kuti, "Sinizawononga chifukwa cha makumi yabili ayo."
32
Anakamba kuti, "Nipempa kuti, musakalipe, Ambuye, ndipo ndipo nizakamba kosiliza. Mwina kapena ni kumi chabe bamene bazapezekamo mwamene muja." Pamene apo anamba kuti, "Sinizawononga chifukwa cha kumi."
33
Ndipo Yehova anaenda njila yake pamene anasiliza kukamba na Abrahamu, na Abrahamu anabwerera kuyenda kunyumba kwake.