1 Ngati mwamuna atenga mukazi nakumukwatila, ngati mukazi sanakondewe mumenso yamwamuna chifukwa apezamo vintu vo sayenelela muli eve, mwaicho afunika kumulembela kalata yosiliza chikwati, naku ika mumanja mwake, nakumupisha munyumba yake. 2 Pamene achoka munyumba yake, angayende nakunkala mukazi wa mwamuna winangu. 3 Ngati mwamuna wachiwiri amuda iye ndikumulembera kalata yothetsera banja, ndikuyiyika mdzanja lake, ndikumutulutsa m'nyumba mwake; kapena ngati wamwalira mwamuna wachiwiriyo, amene adamtenga akhale mkazi wake, 4 pamenepo mwamuna wake woyamba, amene adamchotsa koyamba, asadzamtengenso akhale mkazi wake, atakhala wodetsedwa; popeza ici cinyansa Yehova. Simuyenera kupangitsa kuti dzikolo likhale ndi mlandu, dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti likhale cholowa chanu. 5 Mwamuna akatenga mkazi watsopano, sapita kunkhondo ndi gulu lankhondo, kapena kumulamula kuti akakamize kugwira ntchito iliyonse; adzakhala omasuka kukhala pakhomo kwa chaka chimodzi ndipo azisangalatsa mkazi amene wamutenga. 6 Kulibe mwamuna wamene afunika kutenga chigayo olo mwala wapamwamba ogaila kunkala chogwililako nkongole, chifukwa icho chizankala monga kutenga umoyo wamuntu kunkala monga chogwililako nkongole. 7 Ngati muntu apezeka agwila aliyense pali ba bale bake pali bantu ba Israeli, nakumusunga monga kapolo nakumu gulisa, uyo kawalala afunika kufa; mwaicho muzachosa choipa pakati panu. 8 Samalani ndi nthenda yakhate iliyonse, kuti musamalire ndi kutsatira malangizo onse amene akuphunzitsani ansembe Alevi; monga ndinawalamulira, momwemo muzichita. 9 Kumbukirani chimene Yehova Mulungu wanu anachitira Miriamu pamene munali kutuluka mu Igupto. 10 Ngati wabwelekesa chili chonse kuli munansi wako, usayendeke munyumba yake nakutengelamo chintu. 11 Ufunika kuimilila panja, namuntu wamene unakongolesako azakuletela nkongole yako panja kuli iwe. 12 Ngati ni muntu osauka, sufunika kugona na nkongole yake kunkala na iwe. 13 Ufunika kumubwezela nkongole yake pakugwa kwa kazuba, kuti agone mu chovininkila chake naku ku dalisa; chizankala kulungama kuli iwe pameneso pa Yehova mulungu wako. 14 Osavutisa wanchito ali osauka ndipo ofuna funa, ankale niwabamozi pali ba Israeli, olo pali bakunja bamene bali mumalo yanu mukati mwa muzinda wanu; 15 siku iliyonse mufunika kumupaasa malipilo yake; kasambile kazuba nkani iyi ikalibe kusila, chifukwa ni osauka ndipo abelengela pali malipilo yake. Chitani ichi kuti asakulilileni kuli Yehova, kuti isankale chimo yamene mwachita. 16 Makolowo sayenera kuphedwa chifukwa cha ana awo, kapena ana aphedwe chifukwa cha makolo awo. M'malo mwake, munthu aliyense ayenera kuphedwa chifukwa cha tchimo lake. 17 Musasebebzese mpanvu kuchosapo chilungamo chili choyenelela ku wakunja olo balibe atate bao, olo kutenga chovala cha ofedwa monga malipilo. 18 Koma, mukumbukile kuti munali bakapolo mu Iguputo, ndipo Yehova mulungu wanu anakupulumusani kuchoka kuja. Mwaicho niku onesani imwe kunvelela iyi lamulo 19 Mukamakolola m'munda mwanu, ndipo ngati mwaiwala omeri wa tirigu, musabwerere kukatenga; zikhale za mlendo, za ana amasiye, kapena za mkazi wamasiye, kuti Yehova Mulungu wako akudalitse iwe m'ntchito zonse za manja ako. 20 Mukamagwedeza mtengo wanu wa azitona, musayang'anenso nthambi zake; zikhale za mlendo, za mwana wamasiye, kapena za mkazi wamasiye. 21 Mukakunkha mphesa m'munda wanu wamphesa, musamathenso kukakunkha. Zomwe zatsala zidzakhala za mlendo, za mwana wamasiye, ndi za mkazi wamasiye. 22 Uzikumbukira kuti unali kapolo m'dziko la Iguputo. chifukwa chake ndikukulangizani kuti muzimvera lamuloli