Mutu 14
1
Ndipo Yowabu mwana mwamuna wa Zeruia anaona kuti mutima wa mfumu ufunisisa kuona Abisalomu.
2
Pamene apo Yowabu anatuma mau kuli Tekapri ndipo banauza mukazi wanzelu kuti amulete. Anakamba kuli iye, "Napapata uziapange monga ndiwe wachisoni naka vala vovala vachisoni. Napapata usasizoze iwe mafuta, koma unkale monga mukazi wamene ankala wachisoni ntawi tali pabakufa.
3
Chokonkapo uyende kuli mfumu naku kamba aye pavintu vamene niza ku masulila." Pamene apo Yowabu anamu uza mau yamene azayenda kukamba kuli mfumu.
4
Pamene mukazi wochoka ku Tekoari anakamba na mfumu, anagoneka mutu wake pansi nakukamba kuti, "Nitandizeni ine."
5
Mfumu anakamba kuli, "Nichani chavuta?" Anayanka kuti, "Chazo ona nichakuti ndine mukazi wamasiye, bamuna banga banafa.
6
Ine, wanchito wanu, nenze nabana bamuna babili, benze kumenyana pamozi mu munda, ndiye kunalibe aliyense umozi obapatula benve. Umozi anatema winangu nakumupaya iye.
7
Manje munzi onse wanyamukila pa wanchito wanu, ndiye bakamba kuti, tipaseni mumanja mwatu mwamuna wamene gwesa mubale wake, kuti timu paye, kulipila mubale wake nabo baononge wopyana. Ati baza faka malasha yoshoka yamene nasiya, ndipo sibazasiyila bamuna banga zina kapena mibadwo pa ziko ya pansi."
8
Pamene apo mfumu anakamba namukazi kuti, yenda kunyumba yako, ine niza lamulila chintu chichitiwe pali iwe."
9
Mukazi waku Tekoria anabayanka ba mfumu, "mbuya wanga, mfumu, lekani kulakwa kunkala pali ine napali banja yanga. Mfumu namu pando wachifumu wake osalakwa."
10
Mfumu inayanka kuti, "Aliyense wamene azakamba chilichonse kuli iwe, umulete kuli ine, sazakugwilako futi."
11
Chokonkapo anakamba kuti, Nipempa kuti mfumu iyitane munzelu Yehova Mulungu, kuti obwezela saza yenda pasogolo ku ononga aliyense.
12
Kuchoka apo anakamba kuti, "Nipempa lekani kuti wanchito wanu apitilize kukambako mau kuli mbuya wake mfumu." Anakamba kuti, "Pitiliza kukamba."
13
Pamene apo mukazi anakamba kuti "Nichifukwa nichani munaganiza chintu chaso pa bantu ba Mulungu?
14
Popeza pokamba ichi chinut mfuu ilimonga mutnu wolakwa chifukwa mfumu sinabweze kunyumba futi mwana wake mwanu wamena anapishiwa. Popeza kuti tonse tifunika kufa, ndipo tili monga manzi yamene ta tiliwa pansi, yamene siyanga yolewe futi. Koma Mulungu sazatenga umoyo, mumalo mwake apeza njila yaba bamene bana pishiwa kuti ba bwelele.
15
Manje apa, kuona kuti nabwela kuakamba ici kuli mbuya wanga mfumu, nichifukwa chakuti bantu baniyofya ine. Wanchito wanu azikambisa paeka, 'Nizakamba manje na mfumu. Chizankala kuti amfumu bazachita kupempa kwa wanchito wabo.
16
Kapena mfumu izani mvelela ine naku chosa wanchito wake kuchokela mumanja mwa muna wamene anganiononge ine na mwana wanga mwamuna pamozi, kuchokela pa cholowa chamene Mulungu anatipasa.
17
Chokonkapo wanchito wanu anapempela, 'Yehova, Yehova, Nipempa kuti muleke mau ya mbuya wanga mfumu yoni pulumusa ponkala ngati mungelo wa Mulungu, nimwamene mbuya wanga mfumu alili pokamba chabwino kuchokela ku choipa. Lekani Yehova Mulungu wanu ankalale naimwe."
18
Kuchoka apo mfumu anayanka naku kamba kuli mukazi kuti, "Nipempa usanibise ine chili chonse chamene niza kufunsa." Mukazi anayanka kuti, "Lekani mbuya wanga mfumu ukambe manje."
19
Mfumu inakamba kuti, "sikwanja ya Yowabu yamene ili naiwe muli ivi vonse? Mukazi anayanka nakukamba kuti, "Pamene muli namyoy, mbuya wanga mfumu, kulibe wamene angatabe ku zanja lamanja kapena yakumazele kuonekela kuli vonse vamene mbuya wanga kuli akamba. Ni Yowabu wanchito wanu wamene anilamulila ine vintu vamene wanchito wanu akamba.
20
Wanchito wanu Yowabu achitili ichi ku chinja masantuolidwe ya vamene vichitika. Mbuya wanga alina nzelu, monga nzelu zamu ngelo wa Mulungu, ndipo aziba vonse vamene vichilika mu zika."
21
Pamene apo mfumu anakamba kuli Yowabu kuti, "Ona manje, niza chita ichi chintu. Yenda kansi, ukamulete munyamata mongono Abisalomu abwelele."
22
Pamene apo Yowabu anagwesa mutu wake pansi muku lemekeza naku yamikila kuli mfumu, Yowabu anakamba kuti, lelo wanchito wanu aziba kuti apeza chisomo mu menso yanu, mbuya wanga, mfumu, muli ichi ya chita manga kupempa kwa nchito wake."
23
Pamene apo Yowabu ananyamuka kuyenda ku Gesha, naku leta Abisalomu kumubweza ku Yelusalemu.
24
Ba mfumu banakamba kuti, "Anga bwelele kunyumba yake, koma sanga one chinso changa." Pakunyumba kwake, koma sana one chinso cha mfumu.
25
Manje mu Isilayeli kunalibe wamene enzeli kukambiwa ubwino kuchila pali Abisolamu. Kuchokela kutu kumo wakumendo kufikila kumwamba kumuntu kunalibe choipa pali enve.
26
Ngati ajuba sisi zaka pakusila kwa chaka, chifukwa zinali zolema kuli enve, anali kuzipimisa sisi zake zinali kulema maskekeli yakwanila ngati 200 yamene yanali kupimiwa muchimo chachifumu.
27
Kuli Abisalomu kuna badwa bana bamuna batatu na mukazi umozi, wamene zina yake inali Tama. Enzeli mukazi wabwini maninigi.
28
Abisalomu anankala zaka tu zokwanila mu Yelusalumu, kopanda kuona chinso chamfumu.
29
Chokonkapo Abisalomu anatuma mau kuli Yowabu kumutuma iye kuli mfumu, koma Yowabu sana bwele kuli iye. Ndiye Abisalomu anatuma mau kachibili, koma Yowabu sanabwelele nafuti.
30
Abisalomu anauza banchito bake kuti, "Onani munda wa Yowabu ulipafupi na wanga, elo sama yendako kuja. Yendani naku ushoka."Pamene apo banchito ba Abisalomu bana shoka minda.
31
Kuchoka apo Yowabu ananyamuka nakubwela kuli Abisalomu kunyumba yake, naku kamba kuli enve, "Nichani chamene banchito bako bashokela munda wanga?"
32
Abisalomu anayanka Yowabu kuti, ninatumiza mau kuli iwe kukamba kuti, "bwela kuti nikutume kuli mfumu kukamba kuti, "Nichani chamene nanachiokela ku Gesha? Sembe chankala chabwino kuti nikali kuja. Maje chaichi lekani nione chinso cha mfumu, elo ngati ndine wolakwa, lekani kuti benve bani paye.""
33
Pamene apo Yowabu anayenda kuli mfumu naku iuza. Pamene mfumu anitana Abisalomu, anabwela kwa mfumu naku belamisa pansi pamenso yamfumu, ndipo mfumu ina mupyopyosa Abisalomu.