Mutu 1

1 Moab anapandukila Israyeli ku choka infa ya Ahab. 2 Ndiye Ahaziah anagwa pansi nakuzichita chilonda. Mwaicho anatuma batumiki nakubuza, " Yendani, funsani Baal-zebub, mulungu wa Ekron, ngati chizapola chilonda ichi." 3 Koma mungeli wa Yahwe anakamba kuli Elijah mu Tishbite, " Nyamuka, yenda pamwamba kumana na batumiki ba mfumu baku Samaria, naku bafunsa, kuti muyenda kukumana na Baal-Zebub, mulungu waku Ekron? 4 Mwaicho Yahwe anakamba, " Suzabwela pansi ku choka pa bedi pamene unayenda pamwamba; koma, uzafa ndithu."'" Ndipo Elijah anayenda. 5 Pamene batumiki bana bwelela kuli Ahaziah, anabuza, " Nichani mwa bwelela?" 6 Banakamba kuli eve, " Mwamuna anabwela ku kumana naise anakamba kuli ise, ' Bwelelani kuli mfumu akutumani, na kukamba kuli eve, " Mulungu akamba ivi: ' Nimchifukwa mulibe Mulungu mu Israyeli kuti mutume bamuna kubnvelana na Baal-Zebub, mulungu wa Ekron? Mwaicho Yahwe anakamba, " Suzabwela pansi ku choka pa bedi pamene unayenda pamwamba; koma, uzafa ndithu."'" 7 Ahaiah anakamba kuli batumiki bake, " Enze mwamuna wa bwanji, wamene anabwela pamwamba ku kumana naimwe na ku kuuzani mau aya?" 8 Bana muyanka, " Anavala chopangiwa nasisi ndipo enzeli na belt ya chikumba ku zunguluka mu msana wake. " Mwaicho mfumu anayanka, " Ni Elijah mu Tishbite." 9 Ndiye mfumu anatuma kapteni naba nkondo fifite kuli Elia. Kapten anayenda pamwamba pa lupili pamene anankala Elia. Kapten anakamba kuli eve, "Iwe, mwamuna wa Mulungu, mfumu akamba, ' Bwela pansi.''' 10 Elia anayanka naku kamba kuli kapteni, "Ngati ndine mwamuna wa Mulungu, lekani mulilo ubwele pansi ku shoka iwe nabamuna bali fifite." Ndiye mulilo unabwela pansi ku choka kumwamba naku mu shoka nabamuna bake fifite. 11 Ndiponso mfumu Ahaziah anatuma kapteni winangu naba nkondo bali fifite kuli Elia. Naye kapteni uyu anakamba kuli Elia, "Iwe mwamuna wa Mulungu, mfumu akamba, "Yendesa bwela pansi."' 12 Elia anayanka naku kamba kuli beve, " Ngati ndine mwamuna wa Mulungu, lekani mulilo ubwele pansi ku choka ku mwamba naku kushoka na bamuna bali fifite." Nafuti mulilo wa Mulungu unabwela pansi kuchoka kumwamba naku mushoka naba muna fifite. 13 Nafuti mfumu anatuma gulu ya chitatu yaba nkondo fifite. Uyu kapteni anayenda pamwamba, naku mugwadila pasogolo pa Elia, "Iwe mwamuna wa Mulungu, nikufunsa leka umumoyo wanga na waba nchito bako bali fifite bankale ba bwino pa menso pako. 14 Nicha zoona, mulilo unabwela pansi ku choka ku mwamba naku shoka ma kapteni yabili pamozi na bamuna bao, koma manje leka moyo wanga unkale wabwino mu menso yako." 15 Mungeli wa Yahwe anakamba kuli Elia. "Yenda naye. Osachita mantha." Mwaicho Elia anauka naku yenda naye kuli mfumu. 16 Mukupita kwa nthawi Elia anakamba kuli Ahaziah, " Ivi ndiye vamene Yahwe anakamba, 'Unatuma batumiki ku nvelana na Baal-Zebub, mulungu wa Ekron. Nichifukwa chakuti mulibe Mulungu mu Israyeli kwamenen munga chose nkani? Sopano,siuzabwela pansi ku choka pa bedi pamene unayenda pamwamba; koma, uzafa ndithu.'" 17 Ndiye mfumu Ahaziah anafa monga mwamene mau ya Yahwe yamene anakamba Elia. Joram anayamba kulamulila mumalo yake, mu chaka chachibili cha Jehoram mwana mwamuna wa Jehoshaphat mfumun ya Yuda, chifukwa Ahaziah enzelibe mwana mwamuna. 18 Pa nkani zina za Ahaziah, sizili olembewa mubuku yazochitika za mfumu za Israyeli?