Mutu 14 20

1 Beni-Hadadi mfumu ya Aramu anaunjika bankondo bake bonse pamozi. Panali naye mafumu yangono yangono yali 32, na makavalo na magareta. Anayenda pamwamba,kuzunguluka samaliya na kumenyana nayo 2 . Anatuma ntumi mu muzinda kuli Ahabu mfumu ya Israeli, nakukamba kuli eve, "Ben Hadadi akamba ivi: 3 'Siliva yako na golide yako ni yanga. Kuikilapo futi bakazi bako na bana, babwino maningi, manje ni banga. '" 4 Mfumu ya Israeli inayanka nakukamba ati, "Chili Monga mwamene wakambila, mbuye wanga mfumu. Ine na vonse vamene nilinavo ni vako." 5 ntumi zinabwela futi na kukamba ati, "Ben Hadadi akamba ivi, 'Ninakutumizila mau wokamba kuti unipase siliva yako, golide yako, bakazi bako, na bana bako. 6 Koma nizatuma bantchito banga kuli iwe mailo ntau yamene iyi, ndipo bazasakila sakila munyumba yako na mumanyumba yabanchito bako. Bazagwila na manja yao, nakuchosapo vonse vamene visangalasa menso yako."" 7 Pamene apo mfumu ya Israeli inayitana bakulu bonse ba muziko ija nakukamba ati, "Napapata zibani na kuwona mwamene muntu uyu afunila mavuto. Atumiza utenga kuli ine kuti atenge bakazi banga, bana, siliva na golide, ndipo ine sininamu kanile. " 8 Bakulu bonse na bantu bonse bana kamba kuli Ahabu "Musamumvele kapena kuchita vamene afuna." 9 Pamenepo Ahabu anauza bautenga ba Beni-hadadi kuti, "Uzani mbuye wanga mfumu kuti, 'Nivomeleza pavonse kuti munatumiza kapolo wanu kuchita paulendo woyamba, koma sinizavomela futi .'” ndipo ntumi zinachoka nakupeleka yanko kuli Ben Hadadi. 10 Ndipo Ben Hadadi anatumiza yanko yake kuli Ahabu, nakukamba ati, "Milungu zinichite so chabe nakuchilapo, " ngati milota ya mu samalia ingakwanile bantu bonse bamene banikonka kutengako che mukwanja," 11 Mfumu ya Israeli inayanka nakukamba ati, "Uza Beni-Hadadi kuti, 'Palibe wamene avala zida zake ayenela kuzimvela monga azaivula.'” 12 Ben Hadadi anamvela utenga uwu pamene anali kumwa, eve na mfumu zinali pansi pake zamene zinali mumahema zawo. Ben Hadadi analamula banchito bake kuti, "Konzekelani nkondo." pamene apo banakonzekela mumalo ya nkondo kuti bamenyane na muzinda na muzinda. 13 Ndipo onani, muneneli anabwela kuli Ahabu mfumu ya Israyeli, nakukamba ati, Yehova akamba, ' wayiona gulu yankondo ikulu iyi? Ona, nizayiika mumanja mwako lelo, ndipo uzaziba kuti ndine Yehova. , 14 "Ahabu anayanka kuti, pali ndani?" Yehova anayanka nakukamba ati, "Pali banyamata bosebenzela bakazembe bamalo." Ndipo Ahabu anakamba ati, "Nindani wamene azayamba kumenya nkondo iyi?" Ndipo Yehova anayanka, "Iwe." 15 pamene apo Ahabu anasonkanisa banyamata bamene banalli kusebenzela bakazembe ba mumalo. Banali 232. Kuchoka apo anasonkanisa basilikali bonse, gulu yonse yankondo ya Isiraeli; yokwanila 7000. 16 Banayenda mu zuba. Ben Hadadi enze kumwa moba mutenti yake mpaka kukolewelatu, eve pamozi na mafumu yangonoyangono 32 yamene yenze kumutandiza. 17 Bankondo bafana bamene benzo tumikila bakazembe ba mumalo banayenda pasogolo. Ndipo Ben Hadadi anauziwa na bazondi bamene enze anatuma , "Bamuna bachokela ku Samariya." 18 Ben Hadadi anakamba, "Kaya ngati babwelela mutendele olo nkondo nkondo, baleteni bamoyo." 19 Mwaicho banyamata benzo tumikila bakazembe ba madela banayenda kuchoka mu muzinda ndipo gulu yabankondo inabakonka. 20 Aliyense anapaya muzake. Baku Aaramu banataba ndipo Isiraeli anaba konka pambuyo. Beni-Hadadi mfumu yaku Aramu anataba pakavalo pamozi na bamuna boyendesa makavalo. 21 kuchoka apo mfumu ya Isiraeli inayenda kumenya makavalo na magaleta yao, na kupaya baku Aramu bambili maningi. 22 Manje muneneli anabwela kuli mfumu ya Isilayeli nakukamba kuli yeve," Yenda, ukazilimbise, na kumvesesa na kukonza vameme uchita, chifukwa pakusila kwa chaka mfumu ya Aramu izabwela kumenyana naiwe futi. 23 Banchito ba mfumu ya Aramu banakamba kuli eve, "Mulungu wabo ni Mulungu wa mapili. Ndiye chifukwa chake benze nampamvu kuchila ise. Koma manje tiyeni timenyane nabo muchigwa, ndipo tizankala bolimba kubachila. 24 Mwaicho muchite ivi: Chosani mamfumu yonse pamalo yao yaulamulilo wao nakufakapo bakulu bakulu bankondo. 25 Nyamulani gulu yankondo monga yamene munataya — kavalo mumalo mwa kavalo na galeta mumalo ya galeta- kuti tingamenyane nabo muchigwa. Pamene apo mosakaikila tizankala na mpamvu kubachila . Mwaicho Ben Hadadi anamvela vamene banamuuza na kuchita vamene banamulangiza. 26 Pambuyo poyamba chaka chamanje, Ben Hadadi anasonkanisa ma Aaramu na kuyenda ku Afeki kumenyana na Isirayeli. 27 Bantu baku isilayeli banasonkanisiwa na kupasiwa kuti bamenyane nabo. Bantu baku isilayeli banamanga misasa pasogolo pabo monga tumagulu tubili twa mbuzi, koma ma Aaramu banazula malo yonse. 28 Pamene apo muntu wa Mulungu anabwela pafupi na kukamba na mfumu ya Isirayeli ati, " Yehova akamba: 'Chifukwa ba Aaramu bakamba kuti Yehova ndiye mulungu wa kumapili, koma si Mulungu wa vigwa, nizaika iyi gulu yambili ya nkondo mukwanja yako ndipo uzaziba kuti ndine Yehova."" 29 Mwaicho magulu yankondo yanasonkana moyanganana pa masiku 7. Manje pasiku yasabata nkondo inayamba. Bantu baku isilayeli banapaya basilikali baku Aaramu 100,000 pasiku imozi. 30 Banasala banatabila ku Afeki, mumuzinda, ndipo chipupa chinagwela pali bamuna 27,000 bamene banasala. Ben Hadadi anataba nakuyenda mu muzinda, muchipinda chamukati. 31 Bancito ba Ben Hadadi banakamba kuli eve, "Ona manje, tamvela kuti mfumu za nyumba ya Isirayeli ni mfumu zachifundo.Napapata tiyeni timange vovala vamasaka muchiuno mwatu na ntambo kumitu zatu, na kuyenda kuli mfumu yaku Isirayeli.Mwamwai azapulumusa umoyo wako. " 32 Mwaicho banavala vovala vamasaka muchiuno na ntambo mumitu zao na kuyenda kuli mfumu ya Isirayeli nakukamba ati, "wanchito wanu Ben Hadadi anakamba, 'Napapata lekani ninkale wa moyo.'” Ahabu anakamba, "akali wa moyo? ni mubale wanga. " 33 Manje bamuna banali kumvelela chizindikilo chilichonse chochokela kuli Ahabu, pameneapo mwamusanga banamuyanka kuti, "Ehe, mubale wako Ben Hadadi ali moyo." Mwaicho Ahabu anakamba , " yenda ukamulete." 34 Ndipo Ben-Hadadi anakamba kuli Ahabu, , "Nikubwezelani mizinda zamene batate banga banapoka batate banu, ndipo mungazipangile pogulisila mu Damasiko, mwamene batate banga banachitila ku Samariya." Ahabu anayanka, "Nizakuleka uyende na pangano iyi." ndipo Ahabu anachita naeve pangano, nakumuleka ayende. 35 Muntu winango, umozi pali bana ba baneneli, anakamba kuli munzake kupitila mu mau ya Yehova, "Napapata nimenye." Koma mwamuna anakana kumumenya. 36 Mwaicho muneneli anakamba kuli muneneli munzake, "Chifukwa sunamvele mawu ya Yehova, pamene apo ukanisiya, nkalamu izakupaya." Pamene apo mwamuna anayenda, nkalamu inabwela pali eve na kumupaya. 37 Kuchoka apo muneneli anapeza muntu winango nakukamba, "Napapata nimenye." ndipo mwamuna uyo anamumenya na kumupanga chilonda. 38 Ndipo muneneli anayenda nakuyembekeza mfumu panjila; anali anazibis na nsalu pamenso yake. 39 Pamene mfumu inapitilapo, muneneli analila kuli mfumu nakukamba ati, "Wantchito wako anayenda mukutenta kwa nkondo, ndipo musilikali winanangu ana imilila nakuleta muntu kuli ine na kukamba, 'onani muntu uyu. Ngati mu njila iliyonse asoba, moyo wako uzapasiwa mumalo mwa moyo wake, olo uzafunika kulipila ndalama imozi ya siliva. ' 40 Koma chifukwa wanchito wako enze kungo yenda yenda uku na uku, muntu anataba. " ndipo mfumu ya Israeli inamuwuza kuti, "Ichi ndiye chizankala chilango chako- iwe mwine wake wasanka." 41 Pamene apo muneneli mwamusanga musanga anachosa chomangilila mumenso mwake, ndipo mfumu ya Israeli inazindikila kuti eve enze umozi wa baneneli. 42 Ndipo muneneli anakamba kuli mfumu, Yehova akamba, "Pakuti walekelela muntu wamene nenze nina peleka kuchionongeko, moyo wako uzankala mumalo mwa moyo wake, na bantu mumalo mwa bantu bake. 43 mwaicho Mfumu ya Israeli inayenda kunyumba kwake yokolewa na namkwiyo, nakufika ku Samaliya.