Mutu 3
1
Mobwezela anangenanso musunagoge munali mwamuna anali ndi zanja yofota.
2
Ena anthu anali kumuyangana kuti aone ngati azamucilisa pa sabata kuti amupase mlandu.
3
Yesu anati kuli uja munthu wofota kwanja, " Ima, Imilila pakati pa wonse."
4
Ndipo anati ku anthu, " Kodi ndicovomelekezeka kucita cabwino pa siku ya Sabata kapena kucita cinthu coyipa; kupulumusa moyo, kapena kupaya?" Ndipo onse anali cete.
5
Anabayangana ndi ukali, ana kumudwisiwa ndi kuuma mtima kwawo, ndipo anati kumwamuna, "Tambulula kwanja kwako." Ndipo iye anatambulula, ndi zanja lake linankhala bwino.
6
Ndipo Afalisi panthawi yamene iyo anapita kukafuna-funa njila yompaila pamodzi ndi ma Helodiya.
7
Ndipo Yesu, pamodzi ndi wophunzila , anayenda kuchimana, ndipo anthu ambiri anamukonkha kucokela ku Galileya ndi ku Yudeya
8
ndi kucokela ku Yelusalemu ndi ku Idumeya ndikupitilila Yorodani ndi kuzungulila Tireya ndi Sidoni. Pamene anamvwa pa zamene analikucita, anthu ambiri anaza kwa iye.
9
Ndipo anafunsa wophunzila ake kuti akonzeke kaboti kang'ono chifukwa anthu anali ambili, kuti osati azimuguma-guma.
10
Chifukwa anacilisa ambili, kuti aliyense amene anali wovutika anafuna-funa kuti afike kwa iye kuti amukuze.
11
Nthawi zonse pamene mzimu woipa unamuona iye, unalikugwa pansi ndi kulira kokuwa, unali kunena ati, " Iwe ndiwe Mwana wa Mulungu."
12
Ndipo iye anali kuulesa kuti asamuzibe.
13
Ndipo iye anakwela kulupili, ndi kuyitana aja amene anali kufuna, ndipo anaza kwa iye.
14
Anasankhapo bali twelufu (12), ( awo becipasa zina kuti ndi apositolo), kuti azinkhala naye ndipo kuti akabatume kuyolalikila uthenga.
15
ndi kukala ndi mpamvu zocosela vibanda.
16
Ndipo anasankhapo twelufu: (12) : Simoni uyo wecipasa zina yakuti Petulo;
17
Yakobo mwana wa Zebedayo, and Yohana na mbale wake Yakobo, awo wecipasa zina Bonenge kuthanthauza Bana na kaleza;
18
ndi Anduleya, Filipo, Batolomeyo, Mateyo, Thomase, Yakobo mwana wa Afalesi, Thadeyo, Simoni wa Zilote,
19
ndi Yudasi Iscariyoti, uja wamene emugulisa.
20
Ndipo anayenda kunyumba, ndi anthu ambiri anaza futi pamodzi, ndikukana kudya buledi.
21
Pamene abanja ake anamvwa izi, anayenda kuti akamugwile, cifukwa anati, "waleka kuganiza bwino."
22
Alembi amane anabwela kucokela ku Yelusalemu anati, "ali na vibanda vya Beluzabebu," soti, "mwa ulamulilo wa vibanda ocosa vibanda,"
23
Yesu anabaitana nati kwawo mwafanizo, "Zingacitike bwanji kuti Satana kucosa Satana?
24
Ngati ufumu niwogabanikana suungaimilile.
25
Ngati nyumba niyogabanikana, ila nyumba siingate kuimilila.
26
Ngati Satana waziukila yeka ndipo wagabanikana, sangaimilile, koma uku kukuba kusila kwake.
27
Koma palibe amene angangene munyumba ya nyampamvu nakuba zonse zakeakaliye kumumanga ula nyampamvu, ndipo pambuyo pake niye pombela nyumba yake.
28
29
30
Coonadi ndikuuzani , ucimo uliwonse wa mwana wa munthu uzakakhululukidwa, ndi minyozo yonse yokambidwa, koma aliwonse wonyoza Mzimu Woyela sazakakhululukidwa, koma azankhala wocimwa ndi ucimo wa nthawi zonse." Yesu anakamba izi cifukwa banali kukamba kuti, " Ali na mizimu yonyansa."
31
Ndipo amai ake ndi abale ake anabwela nakuzoimilila panja. Banatuma banthu, nakumuitana.
32
Ndipo anthu ambiri analipo nankhala momuzungulila iye ndipo anati,"Amai anu ndi abale anu ali pabwalo, okusakilani,"
33
Anabayankha nati,"Nanga amai anga ndi abale anga ndibati?"
34
Anayangana aja amene analinkhale omuzunguluka nati,"Onani, aba ndiye amai anga ndi abale anga!
35
Cifukwa aliwonse amene acita cifunilo ca Mlungu, uja munthu ndiye mbale wanga, ndiye mlongo ndipo mai wanga."