Mutu 10
1
Yesu anacoka pamalo paja ndi kupita ku ndela ya Yudeya kumalo yopitilila kamana ka Yolodani, ndipo gulu la anthu linazatso kwa iye. Anali kuwaphunzisatso, wamene unali mwambo wake.
2
Ndipo Afalisi anaza kwa iye kuzamuyesa ndikumufunsa, "Kodi ndicololeka mwamuna kulekana ndi mkazi wake?"
3
Iye anayankha, Kodi Mose analamulila ciani?"
4
Anati, "Mose analola mwamuna kulemba kalata kolekana ndikumpeleka kwawo."
5
"Ici cinali telo cifukwa ca kuuma mitima yanu niye cifukwa cake analemba lamulo yotelo,"
6
Koma kuyambila poyamba kwacilengedwe, 'Mulungu analenga mwamuna ndi mkazi'
7
Pacifukwa ici mwamuna asiye atate ake ndi amai ake ndi kukakangamilana kumkazi wake,
8
ndipo awili azakala thupi imozi.' sono salitso awili, koma umozi mtupi.
9
Niye cifukwa cake camene Mulungu wa ika pamozi, pasankhale munthu wocipatula."
10
Ndipo pamene anali m'nyumba, wophunzila anamfunsa iye nafuti pali ici.
11
Anati kwa iwo, "aliwonse amene aleka mkazi wake ndikukwatila wina amcitila cigololo iye.
12
Ngati anamleka mwamuna wake ndikukakwatiwa ku mwamuna wina, acita cigololo."
13
Ndipo anabwelesa tiana kwa iye kuti atukuze iye, koma wophunzila ake anatuzuzula.
14
Koma pamene Yesu anazindikila ici, anakumdwa nawo ndipo anati kwa iwo, "Tuloleni tiana tize kwa ine, musatulesa, cifukwa ufumu wa Mulungu niwawo awo ngati tiana.
15
Zoonadi ndikuuzani inu, aliyense amene sazalandila ufumu wa Mulungu ngati kamwana kang'ono sazalowa."
16
Ndipo anathenga ana m'manja ake ndikutudalisa pamene anatusanjika manja ake pa tiana.
17
Pamene anayamba ulendo wake, mwamuna wina anamtamangila ndikumgwadila iye, ndikumpempha, "Mphunzisi wabwino, kodi ndicite ciani kuti ningene moyo wosatha?"
18
Yesu anayankha nati, "Kodi niciani uniitana wabwino? kulibe wabwino, kucosako cabe Mulungu.
19
Uziwa malamulo: Usapaye, usacite cigololo, usabe, usacite umboni wa boza, usaname, lemekeza atate ndi amai ako.''
20
Mwamuna uja anati, "Mphunzisi, zinthu izi nankhala womvelela kucokela pamene ninali m'nyamata,"
21
Yesu anamuyangana iye ndi kumkonda iye. Anati kwa iye, "cinthu cimodzi camene usoweka. Ufunika kuti ukagulise katundu wako wonse ndipo ndalama ukapase wosauka, ndipo uzakhala ndi cuma ku mwamba. Ndipo ukabwele ndikunikonkha ine."
22
koma cifukwa ca mau aya anawoneka wosakonda nawo ndipo anacokapo wokumudwisiwa, cifukwa anali ndi cuma cambiri.
23
Yesu anayangana-yangana ndikuuza wophunzila ake nati, "Onani kukosa kwa iwo wolemela kungena ufumu wa Mulungu."
24
Wophunzila ake anadabwa pa mau aya. Koma Yesu analakulanso kwa iwo nati, "Ana, Nikovuta kungena ufumu wa Mulungu!
25
Ciliko capafupi ngamila kungena pamulomo wa nyeleti, kupambana munthu wolemela kungena ufumu wa Mulungu,"
26
Anadabwa kwambiri ndikukambirana wina ndi mzace, "Manje nindani azaphulumuka?"
27
Yesu anawalangana nati, "Kumunthu nicosatheka, koma osati ndi Mulungu. Zinthu zonse ndizotheka ndi Mulungu."
28
Petulo anayamba kukamba naye, " Onani, Tinasiya zonse ndikukukonkhani inu,"
29
Yesu anati, " Zoonadi ndikuuzani inu, palibe amene anasiya nyumba, kapena abale kapena alongo ake, kapena amai ake, kapena atate ake, kapena ana ake kapena malo, cifukwa ca ine m'malo mwa uthenga wa bwino,
30
wamene sazalandila mpaso zopitilila pa hunderedi pano paziko lapansi ; ndi mbale ake, ndi mlongo wake, ndi amake, ndi ana, ndi malo ake, ndikunzunzika, ndiziko likuza, moyo wosatha.
31
koma ambiri amene aliwoyamba azakhala wosiliza, ndi wosiliza azankhala woyamba."
32
33
34
Anali pa njira, yopita ku Yelusalemu, ndipo Yesu anali patsogolo pawo. Wophunzira ake anadabwa, ndipo aja amene analikukonkha anacita mantha. Ndipo Yesu anaitanatso pambali aja twelufu wophunzila ake ndikuwauza zamene zizacitika posacedwa kwa iye. Onani, tilikuyenda kuYelusalemu, Mwana wa Munthu azapelekedwa kwa akulu ansembe ndi alembi. Azaweluzidwa kuti ifa ndikupelekedwa kwa
35
Yakobo ndi Yohane ana a Zebediya anabwela kwa iye anati, ''Mphuzisi, tifuna inu kuti m'tichitire virivotse vamene tizakupemphani."
36
Anakamba kwa iwo anati, Mufuna kuti ine nikucitireni ciani?
37
''Tiloleni kuti tikakhale nayinu muulemelelo wanu, umonzi kuzanjalamanjai ndi wina kulamanzele."
38
Koma Yesu anayankha nati kwa iwo, "Simuziwa camene mukufutsa. kodi mungakwanilitse kumwa mukapu yamene ningamwelemo kapena mungalimbikile ubatizo wamene nizabatizidwa nawo?"
39
Anati kwa iye, "Ndife wokhozeka." Yesu anati kwa iye, "Kapu yamene nizamwelamo, muzamwelamo. Ndipo ndiubatizo wamene ndizabatizidwamo.
40
Koma nkhani yonkhala wina kuzanja lamanja wina lamanzele sindine wamene ningasankhe, koma nikwa iwo amene anakonzekelatu."
41
Pamene ena aja teni wophunzira ake anamvela izi, anakumudwisiwa na Yakobo ndi Yohane.
42
Yesu anawaitana pambali ndi kunena kuti, "Muziwa aja amene wocedwa oweluza a mitundu amawadyakilia iwo, ndi akulu aboma amasewezesa ulamuliro pali iwo.
43
Koma sicizakhala telo pakati kanu. Amene afuna kukhala mkulu pakati kanu afunika kukhala kapolo wa wonse,
44
ndipo aliwonse amene afuna kukhala woyamba pakati kanu akhale wanchito wa wonse.
45
Cifukwa mwana wa munthu sanabwele kuti amutumikire, koma kuti atumikire, ndikupeleka umoyo wake ngati nsembe ku onse."
46
Ndipo anapyamo ku Yeliko. pamene anacoka ku Yeliko ndi wophunzira ake, ndi anthu ambiri, mwana wa Timaulesi, Batulumewo, mpofu yopempha, inakhala panjira.
47
Pamene anamva kuti niYesu waku Nazalete, anayambakukuwa nati, "Yesu , mwana wa Davide, nicitire cifundo!"
48
Ambiri anazuzula mpofu ija, muuzeni kuti akhale cete. koma analirisa, "Mwana wa Davide, nicitilecifundo ine!"
49
Yesu anaimirira ndikulamulira kuti abwele kwake. Anaitana mpofu ija, nati, "Usacite mantha ! ima! alikukuitana.
50
"anataya koti yake, ndikutamanga ndikubwela kwa Yesu.
51
Ndipo Yesu anayankha iye nati, "Kodi ufuna ine nikucitire ciani?"Mpofu ija inati, "Rabbi, nifuna kulandila menso.
52
"Ndipo Yesu anati kwa iye, "Pita. Cikhulupiriro cako cakucilisa."Panthawi yamene ija anayamba kupenyatso, ndipo anamkonkha iye panjira.